Luka 4:38 - Buku Lopatulika38 Ndipo Iye ananyamuka kuchokera m'sunagoge, nalowa m'nyumba ya Simoni. Koma momwemo munali mpongozi wake wa Simoni, anagwidwa ndi nthenda yolimba yamalungo; ndipo anampempha Yesu za iye. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201438 Ndipo Iye ananyamuka kuchokera m'sunagoge, nalowa m'nyumba ya Simoni. Koma momwemo munali mpongozi wake wa Simoni, anagwidwa ndi nthenda yolimba yamalungo; ndipo anampempha Yesu za iye. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa38 Yesu adanyamuka nachoka ku nyumba yamapemphero kuja, nakaloŵa m'nyumba ya Simoni. Apongozi a Simoni ankadwala malungo aakulu, ndipo anthu adapempha Yesu kuti achitepo kanthu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero38 Yesu anatuluka mʼsunagoge ndipo anapita kwa Simoni. Tsopano mpongozi wake wa Simoni amadwala malungo akulu, ndipo anamupempha Yesu kuti amuthandize. Onani mutuwo |