Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 4:20 - Buku Lopatulika

20 Ndipo m'mene Iye anapinda bukulo, nalipereka kwa mnyamata, anakhala pansi; ndipo maso ao a anthu onse m'sunagogemo anamyang'anitsa Iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Ndipo m'mene Iye anapinda bukulo, nalipereka kwa mnyamata, anakhala pansi; ndipo maso ao a anthu onse m'sunagogemo anamyang'anitsa Iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Yesu adatseka bukulo nkulipereka kwa mtumiki wa nyumba yamapemphero, nakhala pansi. Anthu onse amene adaasonkhana m'nyumbamo ankangomupenyetsetsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Kenaka Iye anatseka bukulo, nalibwezera kwa wotumikira ndipo anakakhala pansi. Maso a aliyense mʼsunagogemo anali pa Iye,

Onani mutuwo Koperani




Luka 4:20
13 Mawu Ofanana  

Nthawi yomweyo Yesu anati kwa makamuwo a anthu, Kodi munatulukira kundigwira Ine ndi malupanga ndi mikunkhu, ngati wachifwamba? Tsiku ndi tsiku ndimakhala mu Kachisi kuphunzitsa, ndipo simunandigwire.


nauika m'manda ake atsopano, osemedwa m'mwala, nakunkhunizira mwala waukulu pakhomo pa manda, nachokapo.


ndipo sanapeze chimene akachita; pakuti anthu onse anamlendewera Iye kuti amve.


Ndipo anapereka kwa Iye buku la Yesaya mneneri. Ndipo m'mene Iye adafunyulula bukulo, anapeza pomwe panalembedwa,


Ndipo anayamba kunena kwa iwo, kuti, Lero lembo ili lakwanitsidwa m'makutu anu.


Ndipo Iye analowa m'ngalawa imodzi, ndiyo yake ya Simoni, nampempha iye akankhe pang'ono. Ndipo anakhala pansi m'menemo, naphunzitsa m'ngalawa makamuwo a anthu.


Koma mamawa anadzanso ku Kachisi, ndipo anthu onse anadza kwa Iye; ndipo m'mene anakhala pansi anawaphunzitsa.


Tsiku la Sabata tinatuluka kumuzinda kunka kumbali ya mtsinje, kumene tinaganizira kuti amapempherako; ndipo tinakhala pansi ndi kulankhula ndi akazi amene adasonkhana.


Koma m'mene Petro anachiona, anayankha kwa anthu, Amuna inu a Israele, muzizwa naye bwanji ameneyo? Kapena mutipenyetsetsa ife bwanji, monga ngati tamyendetsa iye ndi mphamvu ya ife eni, kapena ndi chipembedzo chathu?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa