Luka 20:10 - Buku Lopatulika10 Ndipo pa nyengo ya zipatso anatumiza kapolo wake kwa olima mundawo, kuti ampatseko chipatso cha mundawo; koma olimawo anampanda, nambweza wopanda kanthu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Ndipo pa nyengo ya zipatso anatumiza kapolo wake kwa olima mundawo, kuti ampatseko chipatso cha mundawo; koma olimawo anampanda, nambweza wopanda kanthu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 Nyengo yothyola zipatso itafika, munthu uja adatuma wantchito wake kwa alimi aja, kuti akampatsireko zipatso za m'munda muja. Koma alimiwo adammenya, nkumubweza osampatsa kanthu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Pa nthawi yokolola, iye anatumiza wantchito wake kwa alimi aja kuti amupatseko zina mwa zipatso za munda wamphesawo. Koma alimi aja anamumenya namubweza wopanda kanthu. Onani mutuwo |
Ndipo Yehova anachitira umboni Israele ndi Yuda mwa dzanja la mneneri aliyense, ndi mlauli aliyense, ndi kuti, Bwererani kuleka ntchito zanu zoipa, nimusunge malamulo anga ndi malemba anga, monga mwa chilamulo chonse ndinachilamulira makolo anu, ndi kuchitumizira inu mwa dzanja la atumiki anga aneneri.