Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 19:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo m'mene anadza pamalopo Yesu anakweza maso nati kwa iye, Zakeyo, fulumira, nutsike; pakuti lero ndiyenera kukhala m'nyumba mwako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo m'mene anadza pamalopo Yesu anakweza maso nati kwa iye, Zakeyo, fulumira, nutsike; pakuti lero ndiyenera kukhala m'nyumba mwako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Ndiye pamene Yesu adafika pamalopo, adayang'ana m'mwamba, namuuza kuti, “Zakeyo, fulumira, tsika, chifukwa lero ndikuyenera kukakhala nao kunyumba kwako.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Yesu atafika pa malopo, anayangʼana mmwamba ndipo anati kwa iye, “Zakeyu, tsika msangamsanga. Ine ndiyenera kukhala mʼnyumba mwako lero.”

Onani mutuwo Koperani




Luka 19:5
17 Mawu Ofanana  

Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.


Ndipo popita Ine panali iwepo, ndinakuona ulikuvimvinizika m'mwazi mwako. Pamenepo ndinanena ndi iwe m'mwazi wako. Khala ndi moyo, inde ndinati kwa iwe m'mwazi mwako, Khala ndi moyo.


Pakuti Mwana wa Munthu anadza kufunafuna ndi kupulumutsa chotayikacho.


Ndipo taonani, mwamuna wotchedwa dzina lake Zakeyo; ndipo iye anali mkulu wa amisonkho, nali wachuma.


Ndipo anathamanga, natsogola, nakwera mumkuyu kukamuona Iye; pakuti anati apite njira yomweyi.


Ndipo anafulumira, natsika, namlandira Iye wokondwera.


Natanaele ananena naye, Munandidziwira kuti? Yesu anayankha nati kwa iye, Asanakuitane Filipo, pokhala iwe pansi pa mkuyu paja, ndinakuona iwe.


Yesu anayankha nati kwa iye, Ngati wina akonda Ine, adzasunga mau anga; ndipo Atate wanga adzamkonda, ndipo tidzadza kwa iye, ndipo tidzayesa kwa iye mokhalamo.


Ndipo ochita naye pamodzi tidandauliranso kuti musalandire chisomo cha Mulungu kwachabe inu,


kuti Khristu akhale chikhalire mwa chikhulupiriro m'mitima yanu; kuti, ozika mizu ndi otsendereka m'chikondi,


Musaiwale kuchereza alendo; pakuti mwa ichi ena anachereza angelo osachidziwa.


Taona, ndaima pakhomo, ndigogoda; wina akamva mau anga nakatsegula pakhomo, ndidzalowa kwa iye, ndipo ndidzadya naye, ndi iye ndi Ine.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa