Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 19:21 - Buku Lopatulika

21 pakuti ndinakuopani, popeza inu ndinu munthu wouma mtima: munyamula chimene simunachiike pansi, mututa chimene simunachifese.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 pakuti ndinakuopani, popeza inu ndinu munthu wouma mtima: munyamula chimene simunachiika pansi, mututa chimene simunachifesa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Ndinkakuwopani, popeza kuti ndinu munthu wankhwidzi. Mumalonjerera zimene simudaikize, ndiponso mumakolola zimene simudabzale.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Ine ndimakuopani, chifukwa ndinu munthu wowuma mtima. Inu mumatenga chimene simunachiyike ndi kukolola chimene simunadzale.’

Onani mutuwo Koperani




Luka 19:21
16 Mawu Ofanana  

Ndipo wina anadza, nanena, Mbuye, taonani, siyi mina yanu, ndaisunga m'kansalu;


Ananena kwa iye, Pakamwa pako ndikuweruza, kapolo woipa iwe. Unadziwa kuti ine ndine munthu wouma mtima, wonyamula chimene sindinachiike, ndi wotuta chimene sindinachifese;


Pakuti inu simunalandire mzimu wa ukapolo kuchitanso mantha; koma munalandira mzimu wa umwana, umene tifuula nao, kuti, Abba! Atate!


Chifukwa chisamaliro cha thupi chidana ndi Mulungu; pakuti sichigonja ku chilamulo cha Mulungu, pakuti sichikhoza kutero.


Pakuti Mulungu sanatipatse mzimu wa mantha; komatu wa mphamvu ndi chikondi ndi chidziletso.


Pakuti aliyense amene angasunge malamulo onse, koma akakhumudwa pa limodzi, iyeyu wachimwira onse.


Mulibe mantha m'chikondi; koma chikondi changwiro chitaya kunja mantha, popeza mantha ali nacho chilango, ndipo wamanthayo sakhala wangwiro m'chikondi.


kudzachitira onse chiweruziro, ndi kutsutsa osapembedza onse, pa ntchito zao zonse zosapembedza, ndi pa zolimba zimene ochimwa osapembedza adalankhula pa Iye.


Ndipo Samuele ananena kwa anthuwo, Musaope; munachitadi choipa ichi chonse, koma musaleka kutsata Yehova, koma mutumikire Yehova ndi mtima wanu wonse;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa