Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 18:30 - Buku Lopatulika

30 koma adzalandira zobwezedwa koposatu m'nthawi ino; ndipo m'nthawi ilinkudza moyo wosatha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

30 koma adzalandira zobwezedwa koposatu m'nthawi yino; ndipo m'nthawi ilinkudza moyo wosatha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

30 ameneyo pansi pompano adzalandira zonsezo mochuluka kwambiri koposa kale, kenaka kutsogoloko adzalandira moyo wosatha.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

30 adzalephera kulandira mowirikiza mʼmoyo uno, ndi mʼmoyo ukubwerawo, moyo wosatha.”

Onani mutuwo Koperani




Luka 18:30
19 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anachotsa ukapolo wa Yobu, pamene anapempherera mabwenzi ake; Yehova nachulukitsa zake zonse za Yobu mpaka kuziwirikiza.


Mau anu azunadi powalawa ine! Koposa uchi m'kamwa mwanga.


Ndinalandira mboni zanu zikhale cholandira chosatha; pakuti ndizo zokondweretsa mtima wanga.


Chifukwa chake ndikonda malamulo anu koposa golide, inde golide woyengeka.


Ndikondwera nao mau anu, ngati munthu wakupeza zofunkha zambiri.


Chilamulo cha pakamwa panu chindikomera koposa golide ndi siliva zikwizikwi.


Zochepa zake za wolungama zikoma koposa kuchuluka kwao kwa oipa ambiri.


Ndipo aliyense amene anganenere Mwana wa Munthu zoipa, adzakhululukidwa; koma aliyense amene anganenere Mzimu Woyera zoipa sadzakhululukidwa nthawi ino kapena ilinkudzayo.


Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa.


pakuti chizolowezi cha thupi chipindula pang'ono, koma chipembedzo chipindula zonse, popeza chikhala nalo lonjezano la kumoyo uno, ndi la moyo ulinkudza.


Koma chipembedzo pamodzi ndi kudekha chipindulitsa kwakukulu;


Usaope zimene uti udzamve kuwawa; taona, mdierekezi adzaponya ena a inu m'nyumba yandende, kuti mukayesedwe; ndipo mudzakhala nacho chisautso masiku khumi. Khala wokhulupirika kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.


Iye wakukhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Kwa iye wopambana, ndidzampatsa mana obisika, ndipo ndidzampatsa mwala woyera, ndi pamwalawo dzina latsopano lolembedwapo, wosalidziwa munthu aliyense koma iye wakuulandira.


Iye wakupambana, ndidzampatsa akhale pansi ndi Ine pa mpando wachifumu wanga, monga Inenso ndinapambana, ndipo ndinakhala pansi ndi Atate wanga pa mpando wachifumu wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa