Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 17:6 - Buku Lopatulika

6 Koma Ambuye anati, Mukakhala nacho chikhulupiriro ngati kambeu kampiru, mukanena kwa mtengo uwu wamkuyu, Uzulidwe, nuokedwe m'nyanja; ndipo ukadamvera inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Koma Ambuye anati, Mukakhala nacho chikhulupiriro ngati kambeu kampiru, mukanena kwa mtengo uwu wamkuyu, Uzulidwe, nuokedwe m'nyanja; ndipo ukadamvera inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Koma Ambuye adati, “Mukadakhala ndi chikhulupiriro ngakhale chochepa kwambiri ngati kambeu ka mpiru, bwenzi mutauza mkuyu uwu kuti, ‘Zuka, kadzibzale m'nyanja,’ ndipo ukadakumverani ndithu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Yesu anayankha kuti, “Ngati muli ndi chikhulupiriro chachingʼono ngati kambewu kampiru, mukhoza kulamula mtengo wamkuyu uwu kuti, ‘Zulidwa ndi kukadzalidwa mʼnyanja,’ ndipo udzakumverani.

Onani mutuwo Koperani




Luka 17:6
13 Mawu Ofanana  

Ndipo Iye anati, Idza. Ndipo Petro anatsika m'ngalawa, nayenda pamadzi, kufika kwa Yesu.


Ndipo Iye ananena kwa iwo, Chifukwa chikhulupiriro chanu nchaching'ono: pakuti indetu ndinena kwa inu, Mukakhala nacho chikhulupiriro monga kambeu kampiru, mudzati ndi phiri ili, Senderapo umuke kuja; ndipo lidzasendera; ndipo palibe kanthu kadzakukanikani.


Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iwo, Indedi ndinena kwa inu, Ngati mukhala nacho chikhulupiriro, osakayikakayika, mudzachita si ichi cha pa mkuyu chokha, koma ngati mudzati ngakhale kuphiri ili, Tanyamulidwa, nuponyedwe m'nyanja, chidzachitidwa.


Ngati mbeu yampiru, imene ikafesedwa panthaka, ingakhale ichepa ndi mbeu zonse za padziko,


Ndipo Yesu ananena naye, Ngati mukhoza! Zinthu zonse zitheka ndi iye wakukhulupirira.


Ufanana ndi kambeu kampiru, kamene munthu anatenga, nakaponya m'munda wakewake, ndipo kanamera, kanakula mtengo; ndi mbalame za m'mlengalenga zinabindikira mu nthambi zake.


Koma ndani mwa inu ali naye kapolo wolima, kapena woweta nkhosa, amene pobwera iye kuchokera kumunda adzanena kwa iye, Lowa tsopano, khala pansi kudya;


Ndipo anathamanga, natsogola, nakwera mumkuyu kukamuona Iye; pakuti anati apite njira yomweyi.


Ndipo pamene Ambuye anamuona, anagwidwa ndi chifundo chifukwa cha iye, nanena naye, Usalire.


Ndipo Yohane anaitana awiri a ophunzira ake, nawatuma kwa Ambuye, nanena, Kodi ndinu wakudzayo, kapena tiyang'anire wina?


Ndipo ndingakhale ndikhoza kunenera, ndipo ndingadziwe zinsinsi zonse, ndi nzeru zonse, ndipo ndingakhale ndili nacho chikhulupiriro chonse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndilibe chikondi, ndili chabe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa