Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 16:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo mbuye wake anatama kapitao wonyengayo, kuti anachita mwanzeru; chifukwa ana a nthawi ya pansi pano ali anzeru m'mbadwo wao koposa ana a kuunika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo mbuye wake anatama kapitao wonyengayo, kuti anachita mwanzeru; chifukwa ana a nthawi ya pansi pano ali anzeru m'mbadwo wao koposa ana a kuunika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Apo mbuye wa kapitao wonyenga uja adamuyamikira chifukwa cha kuchenjera kwake. Pajatu pokhala ndi anzao, anthu ongokonda zapansipano ngochenjera koposa anthu okhala m'kuŵala kwa Mulungu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 “Bwana anayamikira kapitawo wosakhulupirikayo popeza anachita mochenjera. Pakuti anthu a dziko lino lapansi ndi ochenjera kwambiri akamachita zinthu ndi anthu ofanana nawo kuposa anthu a kuwunika.

Onani mutuwo Koperani




Luka 16:8
23 Mawu Ofanana  

Ndipo njoka inali yochenjera yoposa zamoyo zonse za m'thengo zimene anazipanga Yehova Mulungu. Ndipo inati kwa mkaziyo, Eya! Kodi anatitu Mulungu, Usadye mitengo yonse ya m'mundamu?


Koma Aminoni anali ndi bwenzi lake, dzina lake ndiye Yonadabu, mwana wa Simea, mbale wa Davide. Ndipo Yonadabu anali munthu wochenjera ndithu.


Mundiitanire tsono adze kwa ine aneneri onse a Baala, ompembedza onse, ndi ansembe ake onse, asasowe mmodzi; pakuti ndili nayo nsembe yaikulu yochitira Baala; aliyense wosapenyekapo sadzakhala ndi moyo. Koma Yehu anachichita monyenga, kuti akaononge otumikira Baala.


kwa anthu, ndi dzanja lanu, Yehova, kwa anthu a dziko lapansi pano amene cholowa chao chili m'moyo uno, ndipo mimba yao muidzaza ndi chuma chanu chobisika; akhuta mtima ndi ana, nasiyira ana amakanda zochuluka zao.


Tiyeni, tiwachenjerere angachuluke, ndi kuphatikizana ndi adani athu ikafika nkhondo, ndi kulimbana nafe, ndi kuchoka m'dzikomo.


Munthu amatamandidwa monga mwa nzeru yake; koma wokhota mtima adzanyozedwa.


Ndipo aliyense amene anganenere Mwana wa Munthu zoipa, adzakhululukidwa; koma aliyense amene anganenere Mzimu Woyera zoipa sadzakhululukidwa nthawi ino kapena ilinkudzayo.


Ndipo m'mene iye anati, Kwa akunja, Yesu ananena kwa iye, Chifukwa chake anawo ali aufulu.


Iye amene akhulupirika m'chaching'onong'ono alinso wokhulupirika m'chachikulu; ndipo iye amene ali wosalungama m'chachikulu.


Ndidziwa chimene ndidzachita, kotero kuti pamene ananditulutsa muukapitao, anthu akandilandire kunyumba kwao.


Pomwepo anati kwa wina, Ndipo iwe uli nao mangawa otani? Ndipo uyu anati, Madengu a tirigu zana. Iye ananena naye, Tenga kalata yako nulembere makumi asanu ndi atatu.


Ndipo Ambuye anati, Tamverani chonena woweruza wosalungama.


Ndipo Yesu anati kwa iwo, Ana a dziko lapansi akwatira nakwatiwa:


koma iwo akuyesedwa oyenera kufikira dziko lijalo, ndi kuuka kwa akufa, sakwatira kapena kukwatiwa.


Pokhala muli nako kuunika, khulupirirani kuunikako, kuti mukakhale ana a kuunikako. Izi Yesu analankhula, nachoka nawabisalira.


Munthu asadzinyenge yekha; ngati wina ayesa kuti ali wanzeru mwa inu m'nthawi ino ya pansi pano, akhale wopusa, kuti akakhale wanzeru.


pakuti kale munali mdima, koma tsopano muli kuunika mwa Ambuye; yendani monga ana a kuunika,


chitsiriziro chao ndicho kuonongeka, mulungu wao ndiyo mimba yao, ulemerero wao uli m'manyazi ao, amene alingirira za padziko.


pakuti inu nonse muli ana a kuunika, ndi ana a usana; sitili a usiku, kapena a mdima;


Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa;


M'menemo aoneka ana a Mulungu, ndi ana a mdierekezi: yense wosachita chilungamo siali wochokera mwa Mulungu; ndi iye wosakonda mbale wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa