Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 16:17 - Buku Lopatulika

17 Kuti thambo ndi dziko lapansi zichoke nkwapafupi, koma kuti kalembo kakang'ono kachilamulo kagwe nkwapatali.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Kuti kumwamba ndi dziko lapansi zichoke nkwapafupi, koma kuti kalembo kakang'ono kachilamulo kagwe nkwapatali.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Koma nkwapafupi kuti thambo ndi dziko lapansi zithe, kupambana kuti kalemba kakang'ono ka pa Malamulo kathe mphamvu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Nʼkwapafupi kuti kumwamba ndi dziko lapansi zichoke kulekana ndi kuti kalemba kakangʼono kachoke mʼMalamulo.

Onani mutuwo Koperani




Luka 16:17
11 Mawu Ofanana  

Udzu unyala, duwa lifota, koma mau a Mulungu wathu adzakhala nthawi zachikhalire.


Tukulani maso anu kumwamba, ndipo muyang'ane pansi padziko pakuti kumwamba kudzachoka ngati utsi, ndi dziko lidzatha ngati chofunda, ndipo iwo amene akhala m'menemo adzafa ngati njenjete; koma chipulumutso changa chidzakhala kunthawi zonse, ndi chilungamo changa sichidzachotsedwa.


Pakuti indetu ndinena kwa inu, Kufikira litapitirira thambo ndi dziko, kalemba kakang'ono kamodzi kapena kansonga kake kamodzi sikadzachokera kuchilamulo, kufikira zitachitidwa zonse.


Thambo ndi dziko lapansi zidzapita; koma mau anga sadzapita.


Potero kodi lamulo tiyesa chabe mwa chikhulupiriro? Msatero ai; koma tikhazikitsa lamulo.


koma Mau a Ambuye akhala chikhalire. Ndipo mau olalikidwa kwa inu ndi awo.


Koma tsiku la Ambuye lidzadza ngati mbala; m'mene miyamba idzapita ndi chibumo chachikulu, ndi zam'mwamba zidzakanganuka ndi kutentha kwakukulu, ndipo dziko ndi ntchito zili momwemo zidzatenthedwa.


Ndipo ndinaona, mpando wachifumu waukulu woyera, ndi Iye wakukhalapo, amene dziko ndi m'mwamba zinathawa pamaso pake, ndipo sanapezedwe malo ao.


Ndipo ndinaona m'mwamba mwatsopano ndi dziko latsopano; pakuti m'mwamba moyamba ndi dziko loyamba zidachoka, ndipo kulibenso nyanja.


ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pao; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa