Luka 16:1 - Buku Lopatulika1 Ndipo Iye ananenanso kwa ophunzira ake, Panali munthu mwini chuma, anali ndi kapitao wake; ndipo ameneyu ananenezedwa kwa iye kuti alikumwaza chuma chake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 Ndipo Iye ananenanso kwa ophunzira ake, Panali munthu mwini chuma, anali ndi kapitao wake; ndipo ameneyu ananenezedwa kwa iye kuti alikumwaza chuma chake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Yesu adauza ophunzira ake kuti, “Panali munthu wina wachuma amene anali ndi kapitao wake. Anthu adaadzamneneza kapitaoyo kuti akumwaza chuma cha mbuye wake. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Yesu anawuza ophunzira ake kuti, “Panali munthu wina wachuma amene kapitawo wake anzake anamuneneza kuti amawononga chuma chakecho. Onani mutuwo |
Pamenepo Davide anasonkhanitsa ku Yerusalemu akalonga a Israele, akalonga a mafuko, ndi akulu a zigawo zakutumikira mfumu, ndi akulu a zikwi, ndi akulu a mazana, ndi akulu a zolemera zonse, ndi zoweta zonse za mfumu, ndi ana ake; pamodzi ndi akapitao ndi anthu amphamvu, ndiwo ngwazi zamphamvu onsewo.