Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 15:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo pakupita masiku owerengeka mwana wamng'onoyo anasonkhanitsa zonse, napita ulendo wake kudziko lakutali; ndipo komweko anamwaza chuma chake ndi makhalidwe a chitayiko.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo pakupita masiku owerengeka mwana wamng'onoyo anasonkhanitsa zonse, napita ulendo wake kudziko lakutali; ndipo komweko anamwaza chuma chake ndi makhalidwe a chitayiko.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Patangopita masiku oŵerengeka wamng'ono uja adagulitsa chigawo chake chonse, nachoka kwaoko ndi ndalama zake kupita ku dziko lakutali. Kumeneko adamwaza chuma chakecho ndi mayendedwe oipa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 “Pasanapite nthawi, wamngʼonoyo anasonkhanitsa chuma chake chonse, napita ku dziko lakutali ndipo kumeneko anayamba kumwaza chuma chake mʼnjira zachitayiko.

Onani mutuwo Koperani




Luka 15:13
35 Mawu Ofanana  

Pakuti, taonani, iwo okhala patali ndi Inu adzaonongeka; muononga onse akupembedza kwina, kosiyana ndi Inu.


Wogwira ntchito mwaulesi ndiye mbale wake wa wosakaza.


Wokonda zoseketsa adzasauka; wokonda vinyo ndi mafuta sadzalemera.


Mokhala wanzeru muli katundu wofunika ndi mafuta; koma wopusa angozimeza.


Monga mbalame yosochera kuchisa chake, momwemo munthu wosochera kumalo ake.


Wosunga chilamulo ndiye mwana wozindikira; koma mnzao wa adyera achititsa atate wake manyazi.


Mwamuna wokonda nzeru akondweretsa atate wake; koma wotsagana ndi akazi adama amwaza chuma.


Pakuti ukayamba ndi mkazi wadama, udzamaliza ndi nyenyeswa; ndipo mkazi wa mwini amasaka moyo wa mtengowapatali.


Mtundu wochimwa inu, anthu olemedwa ndi mphulupulu, mbeu yakuchita zoipa, ana amene achita moononga, iwo amsiya Yehova, iwo amnyoza Woyera wa Israele, iwo adana naye nabwerera m'mbuyo.


koma taonani, kukondwa, ndi kusekerera, ndi kupha ng'ombe, ndi kupha nkhosa, ndi kudya nyama, ndi kumwa vinyo; tiyeni tidye ndi kumwa, chifukwa mawa tidzafa.


chokani inu munjira, patukani m'bande, tiletsereni Woyera wa Israele pamaso pathu.


Idzani inu, ati iwo, ndidzatengera vinyo, ndipo tidzakhuta chakumwa chaukali; ndipo mawa kudzakhala monga tsiku lalero, tsiku lalikulu loposa ndithu.


Pakuti anthu anga anachita zoipa ziwiri; anandisiya Ine kasupe wa madzi amoyo, nadziboolera zitsime, zitsime zong'aluka, zosakhalamo madzi.


Mbadwo inu, taonani mau a Yehova. Kodi ndakhala kwa Israele chipululu? Kapena dziko la mdima woti bii? Chifukwa ninji ati anthu anga, Tamasuka sitidzabweranso konse kwa Inu?


atero Yehova, Atate anu apeza chosalungama chanji mwa Ine, kuti andichokera kunka kutali, natsata zachabe, nasanduka achabe?


Anthu anga inu, ndakuchitirani chiyani? Ndakulemetsani ndi chiyani? Chitani umboni wonditsutsa.


ndipo wamng'onoyo anati kwa atate wake, Atate, ndigawirenitu zanga za pa chuma chanu. Ndipo iye anawagawira za moyo wake.


Ndipo pamene anatha zake zonse, panakhala njala yaikulu m'dziko muja, ndipo iye anayamba kusowa.


Koma pamene anadza mwana wanu uyu, wakutha zamoyo zanu ndi akazi achiwerewere, munamphera iye mwanawang'ombe wonenepa.


Ndipo Iye ananenanso kwa ophunzira ake, Panali munthu mwini chuma, anali ndi kapitao wake; ndipo ameneyu ananenezedwa kwa iye kuti alikumwaza chuma chake.


Ndipo panali munthu mwini chuma amavala chibakuwa ndi nsalu yabafuta, nasekera, nadyerera masiku onse;


Koma tsopano mwa Khristu Yesu inu amene munali kutali kale, anakusendezani mukhale pafupi m'mwazi wa Khristu.


ndipo m'mene anadza, analalikira Uthenga Wabwino wa mtendere kwa inu akutali, ndi mtendere kwa iwo apafupi;


ochitidwa zoipa kulipira kwa chosalungama; anthu akuyesera chowakondweretsa kudyerera usana; ndiwo mawanga ndi zilema, akudyerera m'madyerero achikondi ao, pamene akudya nanu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa