Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 14:12 - Buku Lopatulika

12 Ndipo ananenanso kwa iye amene adamuitana, Pamene ukonza chakudya cha pausana kapena cha madzulo, usaitane abwenzi ako, kapena abale ako, kapena a fuko lako, kapena anansi ako eni chuma; kuti kapena iwonso angabwereze kuitana iwe, ndipo udzakhala nayo mphotho.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Ndipo ananenanso kwa iye amene adamuitana, Pamene ukonza chakudya cha pausana kapena cha madzulo, usaitane abwenzi ako, kapena abale ako, kapena a fuko lako, kapena anansi ako eni chuma; kuti kapena iwonso angabwereze kuitana iwe, ndipo udzakhala nayo mphotho.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Yesu adauzanso Mfarisi uja amene adaamuitana kudzadya naye kuti, “Ukamakonza chakudya chamasana kapena chamadzulo, usamaitana abwenzi ako, kapena abale ako, kapena a fuko lako, kapena anzako achuma, chifukwa mwina iwonso adzakuitanako, motero udzalandiriratu mphotho yako.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Kenaka Yesu anati kwa mwini malo uja, “Ukakonza chakudya chamasana kapena chamadzulo, usamayitane abwenzi ako, abale ako, anthu afuko lako kapena anzako achuma; ngati iwe utero, iwo adzakuyitananso, choncho udzalandiriratu mphotho yako.

Onani mutuwo Koperani




Luka 14:12
13 Mawu Ofanana  

Waumphawi adedwa ndi anzake omwe; koma akukonda wolemera achuluka.


Wotsendereza waumphawi kuti achulukitse chuma chake, ndi wopatsa wolemera kanthu, angosauka.


Chifukwa kuti ngati muwakonda akukondana ndi inu mphotho yanji muli nayo? Kodi angakhale amisonkho sachita chomwecho?


Anawakhutitsa anjala ndi zinthu zabwino, ndipo eni chuma anawachotsa opanda kanthu.


Ndipo anansi ake ndi abale ake anamva kuti Ambuye anakulitsa chifundo chake pa iye; nakondwera naye pamodzi.


Chifukwa munthu aliyense wakudzikuza adzachepetsedwa; ndipo wakudzichepetsa adzakulitsidwa.


Koma pamene ukonza phwando uitane aumphawi, opunduka, otsimphina, akhungu;


Ndipo kukhale chibwezero chomwechi (ndinena monga ndi ana anga) mukulitsidwe inunso.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa