Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 14:10 - Buku Lopatulika

10 Koma pamene paliponse waitanidwa iwe, pita nukhale pansi pa malo a kuthungo; kotero kuti pamene akadza iye anakuitana iwe, akanena ndi iwe, Bwenzi langa, sendera, kwera kuno; pomwepo udzakhala ndi ulemerero pamaso pa onse akuseama pachakudya pamodzi ndi iwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Koma pamene paliponse waitanidwa iwe, pita nukhale pansi pa malo a kuthungo; kotero kuti pamene akadza iye anakuitana iwe, akanena ndi iwe, Bwenzi langa, sendera, kwera kuno; pomwepo udzakhala ndi ulemerero pamaso pa onse akuseama pachakudya pamodzi ndi iwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Koma akakuitana, kakhale pa malo otsika, kuti amene adakuitana uja adzakuuze kuti, ‘Bwenzi langa, dzakhale pa malo aulemu pano.’ Apo udzalandira ulemu pamaso pa onse amene uli nao podyera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Koma akakuyitanani, khalani pa malo otsika, kuti amene anakuyitanani uja adzakuwuzeni kuti, ‘Bwenzi, bwera udzakhale pa malo aulemu pano.’ Pamenepo inu mudzalandira ulemu pamaso pa alendo anzanu onse.

Onani mutuwo Koperani




Luka 14:10
5 Mawu Ofanana  

Kuopa Yehova ndiko mwambo wanzeru; ndipo chifatso chitsogolera ulemu.


Ndipo ana aamuna a iwo amene anavuta iwe adzafika, nadzakugwadira; ndipo iwo onse amene anakuchepetsa iwe adzagwadira kumapazi ako, nadzakutcha iwe, Mzinda wa Yehova, Ziyoni wa Woyera wa Israele.


Taona, ndikupatsa ena otuluka m'sunagoge wa Satana akudzinenera okha ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu anama; taona, ndidzawadzetsa alambire pa mapazi ako, nazindikire kuti Ine ndakukonda.


Nati Samuele, M'mene munali wamng'ono m'maso a inu nokha, kodi simunaikidwe mutu wa mafuko a Israele? Ndipo Yehova anakudzozani mfumu ya Israele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa