Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 13:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo Iye ananena fanizo ili: Munthu wina anali ndi mkuyu wooka m'munda wake wampesa. Ndipo anadza nafuna chipatso pa uwu, koma anapeza palibe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo Iye ananena fanizo ili: Munthu wina anali ndi mkuyu wooka m'munda wake wamphesa. Ndipo anadza nafuna chipatso pa uwu, koma anapeza palibe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Yesu adaŵaphera fanizo, adati, “Munthu wina anali ndi mkuyu wobzalidwa m'munda wake wamphesa. Adakafunamo zipatso, koma osazipeza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Kenaka Iye anawawuza fanizo kuti, “Munthu wina anali ndi mtengo wamkuyu, umene anadzala mʼmunda wamphesa, ndipo Iye anapita kukayangʼana zipatso, koma sanazipeze.

Onani mutuwo Koperani




Luka 13:6
14 Mawu Ofanana  

Ndipo Ine ndinakuoka mpesa wangwiro, mbeu yoona; kodi bwanji wandisandukira Ine mbeu yopanda pake, ya mpesa wachilendo?


Kuwatha ndidzawathetsa iwo, ati Yehova, sipadzakhala mphesa pampesa, kapena nkhuyu pamkuyu, ndipo tsamba lidzafota, ndipo zinthu ndinawapatsa zidzawachokera.


Ndinena kwa inu, Iaitu; koma ngati simutembenuka mtima, mudzaonongeka nonse chimodzimodzi.


Ndiponso tsopano lino nkhwangwa yaikidwa pa mizu ya mitengo; chotero mtengo uliwonse wosabala chipatso chabwino udulidwa, nuponyedwa pamoto.


Inu simunandisankhe Ine, koma Ine ndinakusankhani inu, ndipo ndinakuikani, kuti mukamuke inu ndi kubala chipatso, ndi kuti chipatso chanu chikhale; kuti chimene chilichonse mukapempha Atate m'dzina langa akakupatseni inu.


Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro,


Sikunena kuti nditsata choperekacho, komatu nditsata chipatso chakuchulukira ku chiwerengero chanu.


Koma mkuyu unanena nao, Ngati ndidzasiya kuzuna kwanga, ndi zipatso zanga zokoma kukalenga pa mitengo?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa