Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 13:24 - Buku Lopatulika

24 Yesetsani kulowa pa khomo lopapatiza; chifukwa anthu ambiri, ndikuuzani, adzafunafuna kulowamo, koma sadzakhoza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Yesetsani kulowa pa khomo lopapatiza; chifukwa anthu ambiri, ndikuuzani, adzafunafuna kulowamo, koma sadzakhoza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 “Yesetsani kuloŵera pa khomo lophaphatiza, pakuti kunena zoona anthu ambiri adzafuna kuloŵa, koma adzalephera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 “Yesetsani kulowa pa khomo lopapatiza, chifukwa ndikukuwuzani kuti ambiri adzafuna kulowa koma sadzatha kutero.

Onani mutuwo Koperani




Luka 13:24
26 Mawu Ofanana  

Wonyoza afunafuna nzeru osaipeza; koma wozindikira saona vuto m'kuphunzira.


Chifuniro cha waulesi chimupha; chifukwa manja ake akana kugwira ntchito.


Ntchito ya zitsiru izitopetsa zonsezo, pakuti sichidziwa kunka kumzinda.


Ndipo pamene mutambasula manja anu, ndidzakubisirani inu maso anga; inde pochulukitsa mapemphero anu Ine sindidzamva; manja anu adzala mwazi.


Ndipo akudzera monga amadzera anthu, nakhala pansi pamaso pako ngati anthu anga, namva mau ako, koma osawachita; pakuti pakamwa pao anena mwachikondi, koma mtima wao utsata phindu lao.


Ndipo kuyambira masiku a Yohane Mbatizi, kufikira tsopano lino, Ufumu wa Kumwamba uli wokakamizidwa, ndipo okakamirawo aukwatula ndi mphamvu.


Ndipo munthu anati kwa Iye, Ambuye, akupulumutsidwa ndiwo owerengeka kodi? Koma Iye anati kwa iwo,


Koma inu dikirani nyengo zonse, ndi kupemphera, kuti mukalimbike kupulumuka zonse zimene zidzachitika, ndi kuimirira pamaso pa Mwana wa Munthu.


Tiana, katsala kanthawi ndikhala ndi inu. Mudzandifunafuna Ine; ndipo monga ndinanena kwa Ayuda, kuti kumene ndinkako Ine, inu simungathe kudza, momwemo ndinena kwa inu tsopano.


Gwirani ntchito si chifukwa cha chakudya chimene chitayika koma cha chakudya chimene chitsalira kumoyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani inu; pakuti ameneyo Atate, ndiye Mulungu, adamlembera chizindikiro.


Mudzafunafuna Ine, osandipeza; ndipo pomwe ndili Ine, inu simungathe kudzapo.


Pamenepo anatinso kwa iwo; Ndimuka Ine, ndipo mudzandifuna, ndipo m'tchimo lanu mudzafa: kumene ndimukako Ine, simudziwa kudza inu.


Pakuti pakusadziwa chilungamo cha Mulungu, ndipo pofuna kukhazikitsa chilungamo cha iwo okha, iwo sanagonje ku chilungamo cha Mulungu.


kuchita ichi ndidzivutitsa ndi kuyesetsa monga mwa machitidwe ake akuchita mwa ine ndi mphamvu.


Chifukwa chake tichite changu cha kulowa mpumulowo, kuti wina angagwe m'chitsanzo chomwe cha kusamvera.


Ndipo anabwera kwa Yoswa, nati kwa iye, Asakwere anthu onse; koma akwere amuna ngati zikwi ziwiri kapena zitatu kukantha Ai; musalemetsa anthu onse kunkako, pakuti a komweko ndi owerengeka.


Momwemo abale, onjezani kuchita changu kukhazikitsa maitanidwe ndi masankhulidwe anu; pakuti mukachita izi, simudzakhumudwa nthawi zonse;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa