Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 12:52 - Buku Lopatulika

52 pakuti kuyambira tsopano adzakhala m'nyumba imodzi anthu asanu, atatu adzatsutsana ndi awiri, ndi awiri adzatsutsana ndi atatu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

52 pakuti kuyambira tsopano adzakhala m'nyumba imodzi anthu asanu, atatu adzatsutsana ndi awiri, ndi awiri adzatsutsana ndi atatu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

52 Kuyambira tsopano m'banja limodzi mudzakhala anthu asanu ogaŵikana, atatu adzakangana ndi aŵiri, ndipo aŵiri adzakangana ndi atatu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

52 Kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo mʼbanja limodzi mudzakhala anthu asanu ndipo adzawukirana wina ndi mnzake, atatu kuwukira awiri, ndipo awiri kuwukira atatu.

Onani mutuwo Koperani




Luka 12:52
12 Mawu Ofanana  

Ngakhale bwenzi langa lenileni, amene ndamkhulupirira, ndiye amene adadyako mkate wanga, anandikwezera chidendene chake.


Kodi muyesa kuti ndinadzera kudzapatsa mtendere padziko lapansi? Ndinena kwa inu, Iaitu, komatu kutsutsana;


Adzatsutsana atate ndi mwana wake, ndi mwana ndi atate wake; amake adzatsutsana ndi mwana wamkazi, ndi mwana wamkazi ndi amake, mpongozi adzatsutsana ndi mkazi wa mwana wake, ndi mkaziyo ndi mpongozi wake.


Adzakutulutsani m'masunagoge, koma ikudza nthawi imene yense wakupha inu adzayesa kuti atumikira Mulungu.


Ena pamenepo mwa Afarisi ananena, Munthu uyu sachokera kwa Mulungu, chifukwa sasunga Sabata. Koma ena ananena, Munthu ali wochimwa akhoza bwanji kuchita zizindikiro zotere? Ndipo panali kutsutsana mwa iwo.


Ndipo ena anamvera zonenedwazo, koma ena sanamvere.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa