Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 11:51 - Buku Lopatulika

51 kuyambira mwazi wa Abele kufikira mwazi wa Zekariya, amene anamphera pakati pa guwa la nsembe ndi nyumba ya Kachisi. Indetu, ndinena kwa inu udzafunidwa kwa anthu a mbadwo uno.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

51 kuyambira mwazi wa Abele kufikira mwazi wa Zekariya, amene anamphera pakati pa guwa la nsembe ndi nyumba ya Kachisi. Indetu, ndinena kwa inu udzafunidwa kwa anthu a mbadwo uno.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

51 kuyambira kuphedwa kwa Abele, mpaka kuphedwa kwa Zakariya amene adaphedwera m'Nyumba ya Mulungu pakati pa guwa la nsembe ndi malo opatulika kopambana. Ndithu ndikunenetsa kuti anthu amakono adzakhaladi ndi mlandu chifukwa cha ophedwawo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

51 kuyambira magazi a Abele kufikira magazi a Zakariya amene anaphedwa pakati pa guwa lansembe ndi malo opatulika. Inde, Ine ndikuwuzani inu, mʼbado uno udzasenza zonsezi.

Onani mutuwo Koperani




Luka 11:51
9 Mawu Ofanana  

Ndipo anabalanso mphwake Abele. Abele anakhala mbusa wa nkhosa, koma Kaini anali wakulima nthaka.


Ndipo udzati kwa iwo, Umene ndi mtundu wosamvera mau a Yehova Mulungu wao, wosalola kulangizidwa, choonadi chatha, chadulidwa pakamwa pao.


Mwezi wachisanu ndi chitatu, chaka chachiwiri cha Dariusi, mau a Yehova anadza kwa Zekariya mwana wa Berekiya, mwana wa Ido mneneri, ndi kuti,


kotero kuti udzafika pa inu mwazi wonse wotayidwa padziko lapansi, kuyambira kumwazi wa Abele wolungamayo, kufikira kumwazi wa Zekariya mwana wa Barakiya, amene munamupha pakati pa Kachisi ndi guwa la nsembe.


Ndi chikhulupiriro Abele anapereka kwa Mulungu nsembe yoposa ija ya Kaini, imene anachitidwa umboni nayo kuti anali wolungama; nachitapo umboni Mulungu pa mitulo yake; ndipo momwemo iye, angakhale adafa alankhulabe.


ndi kwa Yesu Nkhoswe ya chipangano chatsopano, ndi kwa mwazi wa kuwaza wakulankhula chokoma choposa mwazi wa Abele.


osati monga Kaini anali wochokera mwa woipayo, namupha mbale wake. Ndipo anamupha Iye chifukwa ninji? Popeza ntchito zake zinali zoipa, ndi za mbale wake zolungama.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa