Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 11:19 - Buku Lopatulika

19 Koma ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi Belezebulu, ana anu azitulutsa ndi yani? Mwa ichi iwo adzakhala oweruza anu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Koma ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi Belezebulu, ana anu azitulutsa ndi yani? Mwa ichi iwo adzakhala oweruza anu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Ngati Ineyo ndimatulutsa mizimu yoipa ndi mphamvu za Belezebulu, nanga ophunzira anu amaitulutsa ndi mphamvu za yani? Nchifukwa chake ophunzira anu omwewo ndi amene adzakuweruzani kuti ndinu olakwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Tsopano ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebabu, nanga ophunzira anu amazitulutsa ndi mphamvu ya ndani? Choncho, iwowo ndiye adzakhala oweruza anu.

Onani mutuwo Koperani




Luka 11:19
10 Mawu Ofanana  

Pakamwa pako pakutsutsa, si ine ai. Inde milomo yako ikuchitira umboni wakukutsutsa.


Kumkwanira wophunzira kuti akhale monga mphunzitsi wake, ndi kapolo monga mbuye. Ngati anamutcha mwini banja Belezebulu, sadzaposa kodi kuwatero apabanja ake?


Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa.


Ananena kwa iye, Pakamwa pako ndikuweruza, kapolo woipa iwe. Unadziwa kuti ine ndine munthu wouma mtima, wonyamula chimene sindinachiike, ndi wotuta chimene sindinachifese;


Ndipo Yohane anayankha nati, Ambuye, tinaona wina alikutulutsa ziwanda m'dzina lanu; ndipo tinamletsa, chifukwa satsatana nafe.


Koma Ayuda enanso oyendayenda, otulutsa ziwanda, anadziyesa kutchula pa iwo amene anali ndi ziwanda dzina la Ambuye Yesu, kuti, Ndikulumbirirani pa Yesu amene amlalika Paulo.


Ndipo tidziwa kuti zinthu zilizonse chizinena chilamulo chizilankhulira iwo ali nacho chilamulo; kuti pakamwa ponse patsekedwe, ndi dziko lonse lapansi litsutsidwe ndi Mulungu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa