Luka 11:17 - Buku Lopatulika17 Koma Iye, podziwa zolingirira zao, anati kwa iwo, Ufumu uliwonse wogawanika m'kati mwake upasuka; ndipo nyumba ikagawanika m'kati mwake igwa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201417 Koma Iye, podziwa zolingirira zao, anati kwa iwo, Ufumu uliwonse wogawanika m'kati mwake upasuka; ndipo nyumba ikagawanika m'kati mwake igwa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa17 Koma Yesu adaadziŵa maganizo ao, motero adaŵauza kuti, “Anthu a mu ufumu uliwonse akayamba kuukirana, ufumuwo kutha kwake nkomweko. Ndipo m'banja akayamba kukangana, banjalo limapasuka. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero17 Yesu anadziwa maganizo awo ndipo anawawuza kuti, “Ufumu uliwonse wogawikana udzawonongeka, ndipo nyumba yogawikana idzapasuka. Onani mutuwo |