Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 11:10 - Buku Lopatulika

10 Pakuti yense wakupempha alandira; ndi wofunayo apeza; ndi iye amene agogoda adzamtsegulira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Pakuti yense wakupempha alandira; ndi wofuna apeza; ndi iye amene agogoda adzamtsegulira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Paja munthu amene amapempha, ndiye amalandira, amene amafunafuna, ndiye amapeza, ndipo amene amagogoda, ndiye amamtsekulira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Pakuti aliyense amene amapempha amalandira. Munthu amene amafunafuna amapeza. Iye amene amagogoda amamutsekulira.

Onani mutuwo Koperani




Luka 11:10
12 Mawu Ofanana  

Ndipo ine, pakutenga nkhawa, ndinati, Ndadulidwa kundichotsa pamaso panu. Komatu munamva mau a kupemba kwanga pamene ndinafuulira kwa Inu.


Ndipo ndinati, Mphamvu yanga yatha, osayembekezanso kanthu kwa Yehova.


Inde, pofuula ine ndi kuitana andithandize amakaniza pemphero langa.


Kwa iye wopempha iwe umpatse, ndipo kwa iye wofuna kukukongola usampotolokere.


pakuti yense wakupempha alandira; ndi wakufunayo apeza; ndi kwa wogogodayo chitsegulidwa.


Ndipo ndani wa inu ali atate, mwana wake akadzampempha mkate, adzampatsa mwala? Kapena nsomba, nadzamninkha njoka m'malo mwa nsomba?


Ndipo Ine ndinena ndi inu, Pemphani, ndipo adzakupatsani; funani, ndipo mudzapeza; gogodani ndipo adzakutsegulirani.


Ndipo anawanenera fanizo lakuti ayenera iwo kupemphera nthawi zonse, osafooka mtima;


Mupempha, ndipo simulandira, popeza mupempha koipa, kuti mukachimwaze pochita zikhumbitso zanu.


Taonani tiwayesera odala opirirawo; mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwaona chitsiriziro cha Ambuye, kuti Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa