Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 11:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo kunali, pakukhala Iye pamalo pena ndi kupemphera, m'mene analeka, wina wa ophunzira ake anati kwa Iye, Ambuye, tiphunzitseni ife kupemphera, monganso Yohane anaphunzitsa ophunzira ake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo kunali, pakukhala Iye pamalo pena ndi kupemphera, m'mene analeka, wina wa ophunzira ake anati kwa Iye, Ambuye, tiphunzitseni ife kupemphera, monganso Yohane anaphunzitsa ophunzira ake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Nthaŵi ina Yesu ankapemphera pamalo pena. Pamene adatsiriza, wophunzira wake wina adampempha kuti, “Ambuye, tiphunzitseni kupemphera, monga Yohane Mbatizi adaphunzitsira ophunzira ake.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Tsiku lina Yesu amapemphera pamalo ena. Atamaliza, mmodzi wa ophunzira ake anati kwa Iye, “Ambuye tiphunzitseni kupemphera, monga momwe Yohane anaphunzitsira ophunzira ake.”

Onani mutuwo Koperani




Luka 11:1
14 Mawu Ofanana  

Yehova, mwamva chikhumbo cha ozunzika, mudzakhazikitsa mtima wao, mudzatchereza khutu lanu;


Mau a m'kamwa mwanga ndi maganizo a m'mtima wanga avomerezeke pamaso panu, Yehova, thanthwe langa, ndi Mombolo wanga.


koma chisoweka chinthu chimodzi, pakuti Maria anasankha dera lokoma limene silidzachotsedwa kwa iye.


Ndipo anati kwa iwo, M'mene mupemphera nenani, Atate, Dzina lanu liyeretsedwa; Ufumu wanu udze;


Ndipo kunali masiku awa, Iye anatuluka nanka kuphiri kukapemphera; nachezera usiku wonse m'kupemphera kwa Mulungu.


Ndipo pamene Ambuye anamuona, anagwidwa ndi chifundo chifukwa cha iye, nanena naye, Usalire.


Ndipo Yohane anaitana awiri a ophunzira ake, nawatuma kwa Ambuye, nanena, Kodi ndinu wakudzayo, kapena tiyang'anire wina?


Ndipo kunali, pamene Iye anali kupemphera padera, ophunzira anali naye; ndipo anawafunsa iwo, kuti, Makamuwo a anthu anena kuti Ine ndine yani?


Ndipo pamene padatha ngati masiku asanu ndi atatu atanena mau amenewa, Iye anatenga Petro ndi Yohane ndi Yakobo apite naye, nakwera m'phiri kukapemphera.


Ameneyo, m'masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kumpulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu,


Koma inu, okondedwa, podzimangirira nokha pa chikhulupiriro chanu choyeretsetsa, ndi kupemphera mu Mzimu Woyera,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa