Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 10:28 - Buku Lopatulika

28 Ndipo anati kwa iye, Wayankha bwino; chita ichi, ndipo udzakhala ndi moyo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 Ndipo anati kwa iye, Wayankha bwino; chita ichi, ndipo udzakhala ndi moyo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 Yesu adati, “Mwayankha bwino. Kachiteni zimenezi ndipo mudzakhala ndi moyo.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 Yesu anayankha kuti, “Iwe wayankha bwino, chita zimenezi ndipo udzakhala ndi moyo.”

Onani mutuwo Koperani




Luka 10:28
14 Mawu Ofanana  

ndipo munawachitira umboni, kuti muwabwezerenso ku chilamulo chanu; koma anachita modzikuza, osamvera malamulo anu; koma anachimwira malamulo anu (amene munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo); nakaniza phewa lao, naumitsa khosi lao, osamvera.


Wosunga lamulo asunga moyo wake; wonyalanyaza mayendedwe ake adzafa.


Ndinawapatsanso malemba anga, ndi kuwadziwitsa maweruzo anga, ndiwo munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo.


Koma nyumba ya Israele inapandukira Ine m'chipululu, sanayende m'malemba anga, nanyoza maweruzo anga, amene munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo; ndi masabata anga anawaipsa kwambiri; pamenepo ndidati ndiwatsanulire ukali wanga m'chipululu kuwatha.


Koma anawo anapandukira Ine, sanayende m'malemba anga, kapena kusunga maweruzo anga kuwachita, amene munthu akawachita adzakhala nao ndi moyo; anaipsa masabata anga; pamenepo ndinati ndidzawatsanulira ukali wanga, kuwakwaniritsira mkwiyo wanga m'chipululu.


Inde, muzisunga malemba anga, ndi maweruzo anga; amenewo munthu akawachita, adzakhala nao ndi moyo; Ine ndine Yehova.


Ndipo Iye anati kwa iye, Undifunsiranji za chinthu chabwino? Alipo Mmodzi ndiye wabwino: koma ngati ufuna kulowa m'moyo, sunga malamulo.


Ndipo pakuona kuti anayankha ndi nzeru, Yesu anati kwa iye, Suli kutali ndi Ufumu wa Mulungu. Ndipo palibe munthu analimbanso mtima kumfunsa Iye kanthu.


Simoni anayankha, nati, Ndiyesa kuti, iye amene anamkhululukira zoposa.


Pakuti Khristu ali chimaliziro cha lamulo kulinga kuchilungamo kwa aliyense amene akhulupirira.


Ndipo tidziwa kuti zinthu zilizonse chizinena chilamulo chizilankhulira iwo ali nacho chilamulo; kuti pakamwa ponse patsekedwe, ndi dziko lonse lapansi litsutsidwe ndi Mulungu;


Ndipo lamulo, limene linali lakupatsa moyo, ndinalipeza lakupatsa imfa.


koma chilamulo sichichokera kuchikhulupiriro; koma, Wakuzichita izi adzakhala ndi moyo ndi izi.


Ndipo Yehova anatilamulira tizichita malemba awa onse, kuopa Yehova Mulungu wathu, kuti tipindule nako masiku onse, kuti atisunge amoyo, monga lero lino.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa