Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 1:71 - Buku Lopatulika

71 chipulumutso cha adani athu, ndi padzanja la anthu onse amene atida ife.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

71 chipulumutso cha adani athu, ndi pa dzanja la anthu onse amene atida ife.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

71 Adaalonjeza kuti adzatipulumutsa kwa adani athu, ndi kwa onse odana nafe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

71 chipulumutso kuchoka kwa adani athu ndi kuchoka mʼdzanja la onse otida,

Onani mutuwo Koperani




Luka 1:71
19 Mawu Ofanana  

koma Yehova Mulungu wanu muzimuopa, nadzakulanditsani Iyeyu m'dzanja la adani anu onse.


Ndipo anawapulumutsa m'dzanja la iye amene anawada, nawaombola kudzanja la mdani.


Tipulumutseni, Yehova, Mulungu wathu, ndi kutisokolotsa kwa amitundu, kuti tiyamike dzina lanu loyera, ndi kudzitamandira nacho chilemekezo chanu.


Masiku ake Yuda adzapulumutsidwa, ndipo Israele adzakhala mokhazikika, dzina lake adzatchedwa nalo, ndilo Yehova ndiye chilungamo chathu.


Taonani, ndidzawasokolotsa m'maiko monse, kumene ndinawapirikitsira ndi mkwiyo wanga, ndi m'kupsa mtima kwanga, ndi mu ukali waukulu, ndipo ndidzawabwezeranso kumalo kuno, ndipo ndidzawakhazikitsa mokhulupirika,


Nadzakhalamo osatekeseka, nadzamanga nyumba, ndi kuoka mpesa m'mindamo, nadzakhalamo mosatekeseka, ndikatha kukwaniritsira maweruzo pa onse akuwapeputsa pozungulira pao; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wao.


Ndipo ndidzapangana nazo pangano la mtendere, ndi kuleketsa zilombo zoipa m'dzikomo; ndipo zidzakhala mosatekeseka m'chipululu, ndi kugona kunkhalango.


Ndipo sadzakhalanso chakudya cha amitundu, ndi chilombo chakuthengo sichidzawadyanso; koma adzakhala osatekeseka, opanda wina wakuwaopsa.


Atapita masiku ambiri udzakumbukirika; zaka zotsiriza udzalowa m'dziko lobwezedwa lopulumuka lupanga, losonkhanidwa lituluke m'mitundu yambiri ya anthu, pa mapiri a Israele, amene adakhala achipululu chikhalire; koma litulutsidwa m'mitundu ya anthu, ndipo adzakhala mosatekeseka onsewo.


Wolemekezeka Ambuye, Mulungu wa Israele; chifukwa Iye anayang'ana, nachitira anthu ake chiombolo.


Kutipatsa ife kuti titalanditsidwa kudzanja la adani athu, tidzamtumikira Iye, opanda mantha,


Wodala iwe, Israele; akunga iwe ndani, mtundu wa anthu opulumutsidwa ndi Yehova, ndiye chikopa cha thandizo lako, Iye amene akhala lupanga la ukulu wako! Ndi adani ako adzakugonjera; ndipo udzaponda pa misanje yao.


iye wochita tchimo ali wochokera mwa mdierekezi, chifukwa mdierekezi amachimwa kuyambira pachiyambi. Kukachita ichi Mwana wa Mulungu adaonekera, ndiko kuti akaononge ntchito za mdierekezi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa