Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Luka 1:22 - Buku Lopatulika

22 Koma m'mene iye anatulukamo, sanathe kulankhula nao; ndipo anazindikira kuti iye adaona masomphenya mu Kachisimo. Ndipo iye analinkukodola iwo, nakhalabe wosalankhula.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 Koma m'mene iye anatulukamo, sanatha kulankhula nao; ndipo anazindikira kuti iye adaona masomphenya m'Kachisimo. Ndipo iye analinkukodola iwo, nakhalabe wosalankhula.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Pamene iye adatuluka, sadathe kulankhula nawo. Apo iwo adazindikira kuti m'Nyumbamo waona china chake m'masomphenya. Iye adalankhula nawo ndi manja okha, osathanso kunena mau.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Atatuluka sanathe kuyankhulana nawo. Anazindikira kuti anaona masomphenya mʼNyumbamo, chifukwa ankasonyeza zizindikiro kwa iwo koma sankatha kuyankhula.

Onani mutuwo Koperani




Luka 1:22
8 Mawu Ofanana  

ndipo ndidzamamatiritsa lilime lako kumalakalaka ako, kuti ukhale wosanena, wosawakhalira wakuwadzudzula; pakuti iwo ndiwo nyumba yopanduka.


Ndipo anthu analikulindira Zekariya, nazizwa ndi kuchedwa kwake mu Kachisimo.


Ndipo kunali, pamene masiku a utumiki wake anamalizidwa, anamuka kunyumba kwake.


Ndipo anakodola atate wake, afuna amutche dzina liti?


Pamenepo Simoni Petro anamkodola nanena naye, Utiuze ndiye yani amene anena za iye.


Koma m'mene adawatambasulira dzanja akhale chete, anawafotokozera umo adamtulutsira Ambuye m'ndende. Ndipo anati, Muwauze Yakobo ndi abale izi. Ndipo anatuluka napita kwina.


Ndipo anatulutsa Aleksandro m'khamumo, kumtulutsa iye Ayuda. Ndipo Aleksandro anatambasula dzanja, nafuna kudzikanira kwa anthu adasonkhanawo.


Ndipo m'mene adamlola, Paulo anaimirira pamakwerero, natambalitsira anthu dzanja; ndipo pokhala chete onse, analankhula nao m'chinenedwe cha Chihebri, nanena:


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa