Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 9:4 - Buku Lopatulika

4 ndi ng'ombe, ndi nkhosa yamphongo zikhale zakuyamika, kuziphera nsembe pamaso pa Yehova; ndi nsembe yaufa yosakaniza ndi mafuta; pakuti lero Yehova wakuonekerani inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 ndi ng'ombe, ndi nkhosa yamphongo zikhale zakuyamika, kuziphera nsembe pamaso pa Yehova; ndi nsembe yaufa yosanganiza ndi mafuta; pakuti lero Yehova wakuonekerani inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Mutengenso ng'ombe ndi nkhosa kuti zikhale nsembe zachiyanjano zoti aziphere pamaso pa Chauta. Mubwerenso ndi zopereka za zakudya zosakaniza ndi mafuta, pakuti lero Chauta akuwonekerani.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Mutengenso ngʼombe yayimuna ndi nkhosa yayimuna kuti zikhale nsembe yachiyanjano zoti ziperekedwe pamaso pa Yehova. Pamodzi ndi izi mubwerenso ndi nsembe yachakudya yosakaniza ndi mafuta pakuti lero Yehova akuonekerani.’ ”

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 9:4
18 Mawu Ofanana  

Ndipo kunakhala, pakunena Aroni ndi khamu lonse la ana a Israele kuti iwo anatembenukira kuchipululu, ndipo, taonani, ulemerero wa Yehova unaoneka mumtambo.


Nakonzekeretu tsiku lachitatu; pakuti tsiku lachitatu Yehova adzatsika paphiri la Sinai pamaso pa anthu onse.


Ndipo ulemerero wa Yehova unakhalabe paphiri la Sinai, ndi mtambo unaliphimba masiku asanu ndi limodzi; ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri Iye ali m'kati mwa mtambo anaitana Mose.


Ndipo pamenepo ndidzakomana ndi ana a Israele; ndipo chihema chidzapatulidwa ndi ulemerero wanga.


ndipo taonani, ulemerero wa Mulungu wa Israele unadzera njira ya kum'mawa, ndi mau ake ananga mkokomo wa madzi ambiri, ndi dziko linanyezimira ndi ulemerero wake.


Ndipo atatsiriza masiku, kudzachitika tsiku lachisanu ndi chitatu ndi m'tsogolo, ansembe azichita nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zoyamika paguwalo; ndipo ndidzakulandirani, ati Ambuye Yehova.


Ndipo munthu akabwera nacho chopereka ndicho nsembe yaufa ya kwa Yehova, chopereka chake chizikhala cha ufa wosalala; ndipo athirepo mafuta, ndi kuikapo lubani.


Ndipo chopereka chake chikakhala nsembe yoyamika; akabwera nayo ng'ombe, kapena yaimuna kapena yaikazi, azibwera nayo yopanda chilema pamaso pa Yehova.


Ndipo Mose ndi Aroni analowa ku chihema chokomanako, natuluka, nadalitsa anthu; ndipo ulemerero wa Yehova unaonekera kwa anthu onse.


Nunene kwa ana a Israele, ndi kuti, Dzitengereni tonde akhale nsembe yauchimo; ndi mwanawang'ombe, ndi mwanawankhosa, a chaka chimodzi, opanda chilema, akhale nsembe yopsereza;


Pamenepo anatenga zimene Mose anawauza, napita nazo pakhomo pa chihema chokomanako; ndi msonkhano wonse unasendera kufupi nuimirira pamaso pa Yehova.


Ndipo Mose anati, Ichi ndi chimene Yehova anakuuzani kuti muchichite; ndipo ulemerero wa Yehova udzaonekera kwa inu.


Koma khamu lonse lidati liwaponye miyala. Ndipo ulemerero wa Yehova unaoneka m'chihema chokomanako kwa ana onse a Israele.


Ndipo Kora anasonkhanitsa khamu lonse mopikisana nao ku khomo la chihema chokomanako; ndipo ulemerero wa Yehova unaoneka kwa khamu lonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa