Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 9:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo kunali, tsiku lachisanu ndi chitatu, kuti Mose anaitana Aroni ndi ana ake aamuna, ndi akulu a Israele;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo kunali, tsiku lachisanu ndi chitatu, kuti Mose anaitana Aroni ndi ana ake amuna, ndi akulu a Israele;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Pa tsiku lachisanu ndi chitatu, Mose adaitana Aroni, ana ake ndi atsogoleri a Aisraele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Pa tsiku lachisanu ndi chitatu Mose anayitana Aaroni, ana ake ndi akuluakulu a Aisraeli.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 9:1
9 Mawu Ofanana  

Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu atenge anaankhosa awiri, amuna opanda chilema, ndi mwanawankhosa mmodzi wamkazi wa chaka chimodzi wopanda chilema, ndi atatu a magawo khumi a efa la ufa wosalala ukhale nsembe yaufa, wosakaniza ndi mafuta, ndi muyeso umodzi wa magawo atatu wa mafuta.


Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu abwere nao kwa wansembe, ku khomo la chihema chokomanako, pamaso pa Yehova, kuti ayeretsedwe.


Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu atenge njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, nafike pamaso pa Yehova pa khomo la chihema chokomanako, nazipereke kwa wansembe;


Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu atenge njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, nafike nazo kwa wansembe ku khomo la chihema chokomanako.


Ndipo musatuluka pa khomo la chihema chokomanako masiku asanu ndi awiri, kufikira anakwanira masiku a kudzaza manja kwanu; pakuti adzaze manja anu masiku asanu ndi awiri.


Ndipo Aroni ndi ana ake aamuna anachita zonse zimene Yehova analamula padzanja la Mose.


Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu adze nazo njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, kwa wansembe; ku khomo la chihema chokomanako;


Ndipo popita tsiku la Sabata, mbandakucha, tsiku lakuyamba la sabata, anadza Maria wa Magadala, ndi Maria winayo, kudzaona manda.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa