Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 7:16 - Buku Lopatulika

16 Koma nsembe ya chopereka chake ikakhala ya chowinda, kapena chopereka chaufulu, aidye tsiku lomwelo anabwera nayo nsembe yake; ndipo m'mawa adye chotsalirapo;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Koma nsembe ya chopereka chake ikakhala ya chowinda, kapena chopereka chaufulu, aidye tsiku lomwelo anabwera nayo nsembe yake; ndipo m'mawa adye chotsalirapo;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Koma nsembe yake ikakhala yoti waipereka moilumbirira kapena mwaufulu, aidye pa tsiku lomwe akuiperekalo, ndipo nyama yotsala aidye m'maŵa mwake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 “ ‘Koma ngati nsembe yakeyo apereka chifukwa cha lumbiro kapena mwaufulu, nsembeyo adye tsiku lomwe yaperekedwalo. Koma yotsala angathe kuyidya mmawa mwake.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 7:16
17 Mawu Ofanana  

Ndidzachita zowinda zanga za kwa Yehova, tsopano, pamaso pa anthu ake onse.


Ndidzachita zowinda zanga za kwa Yehova, tsopano, pamaso pa anthu ake onse.


Ndidzalowa m'nyumba yanu ndi nsembe zopsereza, ndidzakuchitirani zowinda zanga,


Amuna ndi akazi onse a ana a Israele amene mitima yao inawafunitsa eni kubwera nazo za ku ntchito yonse imene Yehova analamula ipangike ndi dzanja la Mose, anabwera nacho chopereka chaufulu, kuchipereka kwa Yehova.


nsembe zamtendere zili nane; lero ndachita zowinda zanga.


Ndipo kalonga akapereka chopereka chaufulu nsembe yopsereza, kapena nsembe zoyamika kwa Yehova, amtsegulire pa chipata choloza kum'mawa; ndipo azipereka nsembe yake yopsereza, ndi nsembe zake zoyamika, monga umo amachitira tsiku la Sabata; atatero atuluke; ndipo atatuluka, wina atseke pachipata.


Ng'ombe kapena nkhosa yokula kapena yochepa chiwalo, ikhale nsembe yaufulu; koma pa chowinda siidzalandirika.


Ndipo mukamaphera Yehova nsembe yoyamika, muiphere kuti mulandirike.


pamodzi ndi masabata a Yehova, ndi pamodzi ndi mphatso zanu, ndi pamodzi ndi zowinda zanu zonse, ndi pamodzi ndi zopereka zaufulu zanu, zimene muzipereka kwa Yehova.


Taonani pamapiri mapazi a iye wakulalikira uthenga wabwino, wakubukitsa mtendere! Chita chikondwerero chako, Yuda, kwaniritsa zowinda zako; pakuti wopanda pakeyo sadzapitanso mwa iwe; iye waonongeka konse.


ndipo mukakonzera Yehova nsembe yamoto, nsembe yopsereza, kapena yophera, pochita chowinda cha padera, kapena nsembe yaufulu, kapena nsembe ya pa nyengo zanu zoikika, kumchitira Yehova fungo lokoma, la ng'ombe kapena nkhosa;


Pamenepo padzakhala malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lake, kumeneko muzibwera nazo zonse ndikuuzanizi; nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zophera, magawo anu onse a magawo khumi, ndi nsembe yokweza dzanja lanu, ndi zowinda zanu zosankhika zimene muzilonjezera Yehova.


Simungathe kudya m'mudzi mwanu limodzi la magawo khumi la tirigu wanu, kapena la vinyo wanu, kapena la mafuta anu, kapena oyamba kubadwa a ng'ombe zanu kapena la nkhosa ndi mbuzi zanu, kapena zowinda zanu zilizonse muzilonjeza kapena nsembe zanu zaufulu, kapena nsembe yokweza ya m'dzanja lanu;


Zopatulika zanu zokha zimene muli nazo, ndi zowinda zanu, muzitenge, ndi kupita nazo ku malo amene Yehova adzasankha;


ndi kubwera nazo kumeneko nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zophera, ndi magawo anu onse a magawo khumi, ndi nsembe yokweza ya dzanja lanu, ndi zowinda zanu, ndi nsembe zanu zaufulu, ndi zoyamba kubadwa za ng'ombe zanu, ndi za nkhosa ndi mbuzi zanu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa