Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 6:9 - Buku Lopatulika

9 Uza Aroni ndi ana ake, ndi kuti, Chilamulo cha nsembe yopsereza ndi ichi: nsembe yopsereza izikhala pa nkhuni za paguwa la nsembe usiku wonse kufikira m'mawa; ndipo moto wa paguwa la nsembe uziyakabe pamenepo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Uza Aroni ndi ana ake, ndi kuti, Chilamulo cha nsembe yopsereza ndi ichi: nsembe yopsereza izikhala pa nkhuni za pa guwa la nsembe usiku wonse kufikira m'mawa; ndipo moto wa pa guwa la nsembe uziyakabe pamenepo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 “Ulamule Aroni pamodzi ndi ana ake kuti, ‘Lamulo la nsembe yopsereza kwathunthu ndi ili: nsembeyo izikhala pa moto pa guwa usiku wonse mpaka m'maŵa, ndipo moto wapaguwapowo uzikhala uli chiyakire.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 “Lamula Aaroni ndi ana ake kuti, ‘Lamulo la nsembe yopsereza ndi ili: Nsembe yopserezayo izikhala pa moto pa guwa usiku wonse mpaka mmawa, ndipo moto wa paguwapo uzikhala ukuyaka nthawi zonse.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 6:9
10 Mawu Ofanana  

Ndipo chotsalira cha nsembe yaufa chikhale cha Aroni ndi ana ake; ndicho chopatulika kwambiri cha nsembe zamoto za Yehova.


Ndipo chotsalira cha nsembe yaufa chikhale cha Aroni ndi ana ake; ndicho chopatulika kwambiri cha nsembe zamoto za Yehova.


Ndipo ukhale wa Aroni ndi ana ake, audye pamalo popatulika; pakuti auyese wopatulika kwambiri wochokera ku nsembe zamoto za Yehova; ndilo lemba losatha.


Ndipo Yehova analankhula ndi Mose, nati,


Ndipo Yehova analankhula ndi Mose, nati,


Ndipo unene nao, Nsembe yamoto imene muzibwera nayo kwa Yehova ndiyi: anaankhosa awiri a chaka chimodzi opanda chilema, tsiku ndi tsiku, nsembe yamoto yosalekeza.


Ndipo tsiku la Sabata anaankhosa awiri a chaka chimodzi, opanda chilema, ndi awiri a magawo khumi a efa wa ufa wosalala, ukhale nsembe yaufa, wosakaniza ndi mafuta, ndi nsembe yake yothira;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa