Levitiko 6:10 - Buku Lopatulika10 Ndipo wansembe avale mwinjiro wake wabafuta, navale pathupi pake zovala za pamiyendo zabafuta; naole phulusa, moto utanyeketsa nsembe yamoto paguwa la nsembe, nalitaye m'mphepete mwa guwa la nsembe. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Ndipo wansembe avale mwinjiro wake wabafuta, navale pathupi pake zovala za pamiyendo zabafuta; naole phulusa, moto utanyeketsa nsembe yamoto pa guwa la nsembe, nalitaye m'mphepete mwa guwa la nsembe. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 Tsono wansembe avale mkanjo wake wabafuta, avalenso kabudula wabafuta, ndipo atengeko phulusa la nyama yopsereza pa guwa ndi kulithira pambali pa guwa lomwelo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Tsono wansembe avale mkanjo wake wa nsalu yofewa ndi yosalala. Mʼkati avalenso kabudula wofewa, wosalala. Pambuyo pake atenge phulusa la nyama imene yatenthedwa pa guwa lansembe paja ndi kulithira pambali pa guwa lomwelo. Onani mutuwo |