Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 5:9 - Buku Lopatulika

9 nawazeko mwazi wa nsembe yauchimo pa mbali ya guwa la nsembe; ndi mwazi wotsalira aukamulire patsinde pa guwa la nsembe; ndiyo nsembe yauchimo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 nawazeko mwazi wa nsembe yauchimo pa mbali ya guwa la nsembe; ndi mwazi wotsalira aukamulire patsinde pa guwa la nsembe; ndiyo nsembe yauchimo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 ndipo awazeko magazi a mbalameyo m'mbali mwa guwa. Koma magazi ena otsala aŵathire pansi, kuti ayenderere patsinde pa guwalo. Imeneyo ndiyo nsembe yopepesera machimo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 kenaka awaze magazi a chopereka chopepesera tchimocho mʼmbali mwa guwa. Magazi ena onse awathire pa tsinde la guwa. Imeneyi ndi nsembe yopepesera tchimo.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 5:9
12 Mawu Ofanana  

Chinakondweretsa Yehova chifukwa cha chilungamo chake kukuza chilamulo, ndi kuchilemekeza.


Ndipo wansembe abwere nacho ku guwa la nsembe, namwetule mutu wake, naitenthe paguwa la nsembe; ndi mwazi wake aukamulire pa mbali ya guwa la nsembe,


Pamenepo aiphe ng'ombeyo pamaso pa Yehova; ndipo ana a Aroni, ansembewo, abwere nao mwazi, nawaze mwaziwo pozungulira paguwa la nsembe, lokhala pa khoma la chihema chokomanako.


Naike mwazi wina pa nyanga za guwa la nsembe, lokhala pamaso pa Yehova, lokhala m'chihema chokomanako; nathire mwazi wonse patsinde pa guwa la nsembe yopsereza, lokhala pa khomo la chihema chokomanako.


Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yauchimo ndi chala chake, nauike pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza, ndi kuthira mwazi wake patsinde pa guwa la nsembe yopsereza.


Ndipo wansembe atengeko mwazi ndi chala chake, nauike pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza, ndi kuthira mwazi wake wonse patsinde pa guwa la nsembe.


Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yauchimo ndi chala chake, nauike pa nyanga za guwa la nsembe yopsereza, ndi kuthira mwazi wake wonse patsinde pa guwa la nsembe;


Ndipo wansembeyo atengeko mwazi, nauike pa nyanga za guwa la nsembe la chofukiza cha fungo lokoma, lokhala m'chihema chokomanako pamaso pa Yehova; nathire mwazi wonse wa ng'ombeyo patsinde paguwa la nsembe yopsereza, lokhala pa khomo la chihema chokomanako.


Pamalo pophera nsembe yopsereza ndipo aziphera nsembe yopalamula; nawaze mwazi wake paguwa la nsembe pozungulira.


ndi kwa Yesu Nkhoswe ya chipangano chatsopano, ndi kwa mwazi wa kuwaza wakulankhula chokoma choposa mwazi wa Abele.


Pakuti kunamuyenera Iye amene zonse zili chifukwa cha Iye, ndi zonse mwa Iye, pakutenga ana ambiri alowe ulemerero, kumkonza wamphumphu mtsogoleri woyamba wa chipulumutso chao mwa zowawa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa