Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 5:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo chuma chake chikapanda kufikira nkhosa, wochimwayo adze nayo kwa Yehova nsembe yake yopalamula, njiwa ziwiri, kapena maunda awiri; imodzi ikhale ya nsembe yauchimo, ndi ina ya nsembe yopsereza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo chuma chake chikapanda kufikira nkhosa, wochimwayo adze nayo kwa Yehova nsembe yake yopalamula, njiwa ziwiri, kapena maunda awiri; imodzi ikhale ya nsembe yauchimo, ndi ina ya nsembe yopsereza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 “Koma ngati munthu alibe nkhosa kapena mbuzi, atenge njiŵa ziŵiri kapena nkhunda ziŵiri, kuti zikhale nsembe yopereka kwa Chauta yopepesera machimo ake. Imodzi ikhale nsembe yopepesera machimo, ndipo inayo ikhale nsembe yopsereza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 “ ‘Ngati munthuyo alibe mwana wankhosa, abweretse njiwa ziwiri kapena nkhunda ziwiri kwa Yehova ngati chopereka chopepesera tchimo lake. Imodzi ikhale nsembe yopepesera tchimo, ndipo inayo ikhale nsembe yopsereza.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 5:7
24 Mawu Ofanana  

Ndipo atakwanira masiku a kumyeretsa kwake pa mwana wamwamuna, kapena mwana wamkazi, adze naye mwanawankhosa wa chaka chimodzi ikhale nsembe yopsereza, ndi bunda, kapena njiwa zikhale nsembe yauchimo, ku khomo la chihema chokomanako, kwa wansembe;


Ichi ndi chilamulo cha kwa iye wakubala, kapena mwana wamwamuna kapena wamkazi. Ndipo chuma chake chikapanda kufikira nkhosa, atenge njiwa ziwiri kapena maunda awiri; lina likhale nsembe yopsereza, ndi lina nsembe yauchimo; ndi wansembe amchitire chomtetezera, ndipo adzakhala woyera.


Ndipo iye apereke imodzi ya njiwazo, kapena limodzi la maunda, monga akhoza kufikana nazo,


limodzi la nsembe yauchimo, ndi lina la nsembe yopsereza, pamodzi ndi nsembe yaufa; ndipo wansembe amchitire chomtetezera pamaso pa Yehova iye wakuyeretsedwa.


Ndipo wansembe apereke limodzi likhale nsembe yauchimo, ndi linalo likhale nsembe yopsereza; ndipo wansembe amchitire chomtetezera pamaso pa Yehova chifukwa cha kukha kwake komdetsa.


Ndipo ku khamu la ana a Israele atenge atonde awiri akhale a nsembe yauchimo, ndi nkhosa yamphongo imodzi ikhale ya nsembe yopsereza.


Koma chuma chake chikapanda kufikira kuyesa kwako, amuike pamaso pa wansembe, kuti wansembeyo amuyese; ndipo wansembeyo amuyese, monga akhoza iye amene anawinda.


Koma chuma chake chikapanda kufikira njiwa ziwiri kapena maunda awiri, wochimwayo azidza nacho chopereka chake limodzi la magawo khumi la efa la ufa wosalala, likhale la nsembe yauchimo; asamaikapo mafuta, kapena kuikapo lubani ai; pakuti ndicho nsembe yauchimo.


Ndipo chilamulo cha nsembe yopalamula ndi ichi: ndiyo yopatulika kwambiri.


Nunene kwa ana a Israele, ndi kuti, Dzitengereni tonde akhale nsembe yauchimo; ndi mwanawang'ombe, ndi mwanawankhosa, a chaka chimodzi, opanda chilema, akhale nsembe yopsereza;


Nena ndi ana a Israele, ndi kuti Mwamuna kapena mkazi akachita tchimo lililonse amachita anthu, kuchita mosakhulupirika pa Yehova, nakapalamuladi;


Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu adze nazo njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, kwa wansembe; ku khomo la chihema chokomanako;


ndipo wansembe akonze imodzi nsembe yauchimo, ndi ina nsembe yopsereza, namtetezere popeza anachimwa nao mtembowo; ndipo apatulire mutu wake tsiku lomwelo.


Taonani, Ine ndikutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu; chifukwa chake khalani ochenjera monga njoka, ndi oona mtima monga nkhunda.


Ndipo Yesu analowa ku Kachisi wa Mulungu natulutsira kunja onse akugulitsa ndi kugula malonda, nagubuduza magome a osintha ndalama, ndi mipando ya ogulitsa nkhunda;


Ndipo Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anatuluka m'madzi: ndipo onani, miyamba inamtsegukira Iye, ndipo anapenya Mzimu wa Mulungu wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa Iye;


ndi kukapereka nsembe monga mwanenedwa m'chilamulo cha Ambuye, njiwa ziwiri, kapena maunda awiri.


Pakuti ngati chivomerezocho chili pomwepo, munthu alandiridwa monga momwe ali nacho, si monga chimsowa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa