Levitiko 5:12 - Buku Lopatulika12 Ndipo adze nacho kwa wansembe, ndi wansembeyo atengeko wodzala manja ukhale chikumbutso chake, nachitenthe paguwa la nsembe monga umo amachitira nsembe zamoto za Yehova; ndiyo nsembe yauchimo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201412 Ndipo adze nacho kwa wansembe, ndi wansembeyo atengeko wodzala manja ukhale chikumbutso chake, nachitenthe pa guwa la nsembe monga umo amachitira nsembe zamoto za Yehova; ndiyo nsembe yauchimo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa12 Tsono abwere ndi ufa kwa wansembe, ndipo wansembeyo atapeko wa dzanja limodzi ngati chikumbutso ndi kuutenthera pa guwa, pamodzi ndi nsembe zopereka kwa Chauta. Imeneyi ndiyo nsembe yopepesera machimo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero12 Abweretse ufawo kwa wansembe ndipo wansembeyo atapeko dzanja limodzi kuti ukhale ufa wachikumbutso ndi kuwutentha pa guwa pamodzi ndi chopereka chopsereza kwa Yehova. Imeneyi ndi nsembe yopepesera tchimo. Onani mutuwo |