Levitiko 5:11 - Buku Lopatulika11 Koma chuma chake chikapanda kufikira njiwa ziwiri kapena maunda awiri, wochimwayo azidza nacho chopereka chake limodzi la magawo khumi la efa la ufa wosalala, likhale la nsembe yauchimo; asamaikapo mafuta, kapena kuikapo lubani ai; pakuti ndicho nsembe yauchimo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201411 Koma chuma chake chikapanda kufikira njiwa ziwiri kapena maunda awiri, wochimwayo azidza nacho chopereka chake limodzi la magawo khumi la efa la ufa wosalala, likhale la nsembe yauchimo; asamaikapo mafuta, kapena kuikapo lubani ai; pakuti ndicho nsembe yauchimo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa11 “Ngati munthu alibe njiŵa ziŵiri kapena nkhunda ziŵiri, abwere ndi ufa wosalala wokwanira muyeso wa kilogaramu limodzi, kuti ukhale nsembe yopepesera tchimo limene wachita. Asathireko mafuta kapenanso lubani, chifukwa imeneyi ndi nsembe yopepesera machimo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero11 “ ‘Koma ngati munthuyo alibe njiwa ziwiri kapena nkhunda ziwiri, abweretse ufa wosalala wokwanira kilogalamu imodzi kuti ukhale chopereka chopepesera tchimo limene wachita. Asathiremo mafuta kapena lubani chifukwa ndi chopereka chopepesera tchimo. Onani mutuwo |