Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 4:3 - Buku Lopatulika

3 akalakwa wansembe wodzozedwa ndi kupalamulira anthu; pamenepo azibwera nayo kwa Yehova ng'ombe yamphongo, yopanda chilema, chifukwa cha kuchimwa kwake adakuchita, ikhale nsembe yauchimo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 akalakwa wansembe wodzozedwa ndi kupalamulira anthu; pamenepo azibwera nayo kwa Yehova ng'ombe yamphongo, yopanda chilema, chifukwa cha kuchimwa kwake adakuchita, ikhale nsembe yauchimo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 wochimwayo akakhala wansembe wodzozedwa, pakutero wausandutsa wopalamula mpingo wonse, tsono azipereka kwa Chauta ng'ombe yaing'ono yamphongo yopanda chilema, chifukwa cha tchimo lakelo. Imeneyo ndiyo nsembe yopepesera machimo ake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 “ ‘Ngati wansembe wodzozedwa achimwa, ndi kuchimwitsa anthu onse, iyeyu ayenera kupereka mwana wangʼombe wamphongo wopanda chilema chifukwa cha tchimo limene wachitalo. Imeneyi ndi nsembe ya Yehova yopepesera tchimo lake.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 4:3
32 Mawu Ofanana  

Ndipo anabwera nazo ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri ndi anaankhosa asanu ndi awiri, ndi atonde asanu ndi awiri, zikhale nsembe yauchimo ya ufumu, ndi ya malo opatulika, ndi ya Yuda. Ndipo anawauza ansembe ana a Aroni azipereke paguwa la nsembe la Yehova.


Otengedwa ndende, atatuluka m'ndende, anapereka nsembe zopsereza kwa Mulungu wa Israele, ng'ombe khumi ndi ziwiri za Aisraele onse, nkhosa zamphongo makumi asanu ndi anai mphambu zisanu ndi imodzi, anaankhosa makumi asanu ndi awiri mphambu asanu ndi awiri, atonde khumi ndi awiri, akhale nsembe yazolakwa; zonsezi ndizo nsembe yopsereza ya kwa Yehova.


Koma nyama ya ng'ombeyo, ndi chikopa chake, ndi chipwidza chake, uzitentha izi ndi moto kunja kwa chigono; ndiyo nsembe yauchimo.


Ndipo utapeko pamwazi uli paguwa la nsembe, ndi pa mafuta akudzoza nao, ndi kuwaza pa Aroni, ndi pa zovala zake, ndi pa ana ake aamuna, ndi pa zovala za ana ake aamuna, pamodzi ndi iye; kuti akhale wopatulidwa, ndi zovala zake zomwe, ndi ana ake aamuna ndi zovala zao zomwe pamodzi ndi iye.


Pamenepo utenge mafuta odzoza nao nuwatsanulire pamutu pake, ndi kumdzoza.


Ndipo Aroni azichita choteteza pa nyanga zake kamodzi m'chaka; alichitire choteteza ndi mwazi wa nsembe yauchimo ya choteteza, mwa mibadwo yanu; ndilo lopatulika kwambiri la Yehova.


Ndipo m'khonde la pachipata munali magome awiri chakuno, ndi magome awiri chauko, kuti apherepo nsembe yopsereza, ndi nsembe yauchimo, ndi nsembe yopalamula.


Upatse ansembe Alevi, a mbeu za Zadoki, okhala pafupi ndi Ine, kunditumikira Ine, ati Ambuye Yehova, mwanawang'ombe, akhale wa nsembe yauchimo.


Ndipo tsiku loti alowa m'malo opatulika, bwalo lam'kati, kutumikira m'malo opatulika, apereke nsembe yake yauchimo, ati Ambuye Yehova.


Ndipo chopereka chake chikakhala cha nkhosa, kapena cha mbuzi, chikhale nsembe yopsereza; azibwera nayo yaimuna yopanda chilema.


Chopereka chake chikakhala nsembe yopsereza ya ng'ombe, azibwera nayo yaimuna yopanda chilema; abwere nayo ku khomo la chihema chokomanako, kuti alandirike pamaso pa Yehova.


Ndipo Aroni abwere nayo ng'ombe ya nsembe yauchimo, ndiyo yakeyake, nadzitetezere iye yekha, ndi mbumba yake, ndi kupha ng'ombe ya nsembe yauchimo ndiyo yakeyake;


Aroni azilowa pa bwalo la malo opatulika nazozo: ng'ombe yamphongo ikhale ya nsembe yauchimo, ndi nkhosa yamphongo ikhale ya nsembe yopsereza.


Ndipo ku khamu la ana a Israele atenge atonde awiri akhale a nsembe yauchimo, ndi nkhosa yamphongo imodzi ikhale ya nsembe yopsereza.


Ndipo Aroni abwere nayo ng'ombe ya nsembe yauchimo, ndiyo yakeyake, nachite chodzitetezera iye yekha, ndi mbumba yake.


kukadziwika kuchimwa adachimwako, pamenepo msonkhano uzibwera nayo ng'ombe yamphongo, ikhale nsembe yauchimo, ndipo udze nayo ku khomo la chihema chokomanako.


akamdziwitsa kuchimwa kwake adachimwako, azidza nacho chopereka chake, ndicho tonde wopanda chilema;


akamdziwitsa kuchimwa kwake adachimwako, azidza nacho chopereka chake mbuzi yaikazi, yopanda chilema, chifukwa cha kuchimwa kwake adakuchita.


Ndipo wansembe wodzozedwayo atengeko mwazi wa ng'ombeyo, nabwere nao ku chihema chokomanako;


nadze nayo nsembe yopalamula kwa Yehova chifukwa cha kulakwa kwake adachimwira, ndiyo nkhosa yaikazi, kapena mbuzi yaikazi, ikhale nsembe yauchimo; ndipo wansembe amchitire chomtetezera chifukwa cha kuchimwa kwake.


Amuna onse a mwa ana a Aroni adyeko, ndilo lemba losatha la ku mibadwo yanu, chiwachokere ku nsembe zamoto za Yehova; aliyense wakuzikhudza izi adzakhala wopatulika.


Ndipo anatsanulirako mafuta odzoza pamutu pa Aroni, namdzoza kumpatula.


ndipo anati kwa Aroni, Dzitengere mwanawang'ombe wamwamuna, akhale nsembe yauchimo, ndi nkhosa yamphongo ikhale nsembe yopsereza, zopanda chilema, nubwere nazo pamaso pa Yehova.


Nunene kwa ana a Israele, ndi kuti, Dzitengereni tonde akhale nsembe yauchimo; ndi mwanawang'ombe, ndi mwanawankhosa, a chaka chimodzi, opanda chilema, akhale nsembe yopsereza;


Ndipo anagwa nkhope zao pansi, nati, Mulungu, ndinu Mulungu wa mizimu ya anthu onse, walakwa munthu mmodzi, ndipo kodi mukwiya nalo khamu lonse?


Pamenepo atenge ng'ombe yamphongo ndi nsembe yake yaufa, ufa wosakaniza ndi mafuta; utengenso ng'ombe yamphongo ina ikhale nsembe yauchimo.


Pakuti chimene chilamulo sichinathe kuchita, popeza chinafooka mwa thupi, Mulungu anatumiza Mwana wake wa Iye yekha m'chifanizo cha thupi la uchimo, ndi chifukwa cha uchimo, natsutsa uchimo m'thupi;


Ameneyo sanadziwe uchimo anamyesera uchimo m'malo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye.


ndipo chifukwa chakecho ayenera, monga m'malo a anthuwo, moteronso m'malo a iye yekha, kupereka nsembe chifukwa cha machimo.


kapena mwa mwazi wa mbuzi ndi anaang'ombe, koma mwa mwazi wa Iye yekha, analowa kamodzi kumalo opatulika, atalandirapo chiombolo chosatha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa