Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 3:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo aike dzanja lake pamutu wa chopereka chake, ndi kuipha pa chipata cha chihema chokomanako; ndipo ana a Aroni, ansembewo, awaze mwazi wake paguwa la nsembe pozungulira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo aike dzanja lake pa mutu wa chopereka chake, ndi kuipha pa chipata cha chihema chokomanako; ndipo ana a Aroni, ansembewo, awaze mwazi wake pa guwa la nsembe pozungulira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Munthuyo asanjike dzanja lake pamutu pa ng'ombeyo, ndipo aiphere pa khomo la chihema chamsonkhano. Pomwepo ansembe, ana a Aroni, aliwaze magazi guwa molizungulira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Munthuyo asanjike dzanja lake pamutu pa ngʼombeyo, ndipo ayiphere pa khomo la tenti ya msonkhano. Ndipo ansembe, ana a Aaroni, awaze magazi mbali zonse za guwalo.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 3:2
23 Mawu Ofanana  

Ndipo ubwere nayo ng'ombe yamphongo patsogolo pa chihema chokomanako; ndipo Aroni ndi ana ake aamuna aike manja ao pamutu pa ng'ombe yamphongoyo.


Nuphe ng'ombe yamphongoyo pamaso pa Yehova, pa khomo la chihema chokomanako.


Utengenso nkhosa yamphongo imodziyo; ndi Aroni ndi ana ake aamuna aike manja ao pamutu pa nkhosa yamphongoyo.


Nuiphe nkhosa yamphongoyo, ndi kutenga mwazi wake, ndi kuuwaza paguwa la nsembe pozungulira.


Ndipo utenge nkhosa yamphongo yinayo; ndi Aroni ndi ana ake aamuna aike manja ao pamutu pa nkhosa yamphongoyo.


Tonse tasochera ngati nkhosa; tonse tayenda yense m'njira ya mwini yekha; ndipo Yehova anaika pa Iye mphulupulu ya ife tonse.


Ndipo aiphere iyo pa mbali ya kumpoto ya guwa la nsembe, pamaso pa Yehova; ndipo ana a Aroni, ansembewo, awaze mwazi wake paguwa la nsembe pozungulira.


Munthu aliyense wa mbumba ya Israele akapha ng'ombe, kapena mwanawankhosa, kapena mbuzi, m'chigono, kapena akaipha kunja kwa chigono,


osadza nayo ku khomo la chihema chokomanako, kuti aipereke chopereka cha Yehova, ku bwalo la Kachisi wa Yehova; azimuyesa munthuyu wochimwira mwazi, wakhetsa mwazi; ndipo amsadze munthuyo kumchotsa pakati pa anthu a mtundu wake;


Pamenepo abwere nayo nsembe yamoto ya kwa Yehova, yotengako ku nsembe yoyamika; achotse mafuta akukuta matumbo, ndi mafuta onse akukhala pamatumbo,


naike dzanja lake pamutu pa chopereka chake, naiphe patsogolo pa chihema chokomanako; ndipo ana a Aroni awaze mwazi wake paguwa la nsembe pozungulira.


Ndipo anabwera nayo nkhosa yamphongo yinayo, ndiyo mphongo ya kudzaza manja; ndipo Aroni ndi ana ake aamuna anaika manja ao pamutu wa mphongoyo.


Ndipo ndidzatsanulira pa nyumba ya Davide, ndi pa okhala mu Yerusalemu, mzimu wa chisomo ndi wakupembedza; ndipo adzandipenyera Ine amene anandipyoza; nadzamlira ngati munthu alira mwana wake mmodzi yekha, nadzammvera zowawa mtima, monga munthu amvera zowawa mtima mwana wake woyamba.


Koma ng'ombe yoyamba kubadwa, kapena nkhosa yoyamba kubadwa, kapena mbuzi yoyamba kubadwa, usaziombola; ndizo zopatulika; uwaze mwazi wake paguwa la nsembe, ndi kufukiza mafuta ao, nsembe yamoto ya fungo lokoma kwa Yehova.


ndipo munamupha Mkulu wa moyo; amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa; za ichi ife tili mboni.


Kuyambira ndi inu, Mulungu, ataukitsa Mwana wake, anamtuma kukudalitsani inu, ndi kukubwezani yense ku zoipa zake.


Ameneyo sanadziwe uchimo anamyesera uchimo m'malo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa