Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 3:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo chopereka chake chikakhala nsembe yoyamika; akabwera nayo ng'ombe, kapena yaimuna kapena yaikazi, azibwera nayo yopanda chilema pamaso pa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo chopereka chake chikakhala nsembe yoyamika; akabwera nayo ng'ombe, kapena yaimuna kapena yaikazi, azibwera nayo yopanda chilema pamaso pa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 “Ngati munthu apereka nsembe yachiyanjano kwa Chauta, nsembe yake ikakhala ya ng'ombe yamphongo kapena yaikazi, ikhale yopanda chilema.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 “ ‘Ngati munthu apereka nsembe ya chiyanjano kwa Yehova, ndipo choperekacho nʼkukhala ngʼombe yayimuna kapena yayikazi, ikhale yopanda chilema.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 3:1
29 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide anamangira Yehova guwa la nsembe komweko; napereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zoyamika, naitana kwa Yehova; ndipo anamyankha ali m'mwamba ndi moto paguwa la nsembe yopsereza.


Undiumbire guwa la nsembe ladothi, nundiphere pomwepo nsembe zako zopsereza, ndi nsembe zako zamtendere, nkhosa zako ndi ng'ombe zako; paliponse ndikumbukiritsa anthu dzina langa ndidzakudzera ndi kukudalitsa.


Ndipo anatuma ana a Israele a misinkhu ya anyamata, ndiwo anapereka nsembe zopsereza, naphera Yehova nsembe zamtendere, za ng'ombe.


ndipo zikhale za Aroni ndi za ana ake aamuna, mwa lemba losatha, ziwadzere kwa ana a Israele; popeza ndiyo nsembe yokweza; ndipo ikhale nsembe yokweza yodzera kwa ana a Israele, ya kwa nsembe zamtendere zao, ndiyo nsembe yao yokweza ya Yehova.


nsembe zamtendere zili nane; lero ndachita zowinda zanga.


Ndipo atatsiriza masiku, kudzachitika tsiku lachisanu ndi chitatu ndi m'tsogolo, ansembe azichita nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zoyamika paguwalo; ndipo ndidzakulandirani, ati Ambuye Yehova.


ndi mwanawankhosa mmodzi wa zoweta, kumtenga pa mazana awiri wochokera kumadimba a Israele, ndiye wa nsembe yaufa, ndi wa nsembe yopsereza, ndi wa nsembe zoyamika, kuwachitira chotetezera, ati Ambuye Yehova.


Ndipo chopereka chake chikakhala cha nkhosa, kapena cha mbuzi, chikhale nsembe yopsereza; azibwera nayo yaimuna yopanda chilema.


Chopereka chake chikakhala nsembe yopsereza ya ng'ombe, azibwera nayo yaimuna yopanda chilema; abwere nayo ku khomo la chihema chokomanako, kuti alandirike pamaso pa Yehova.


kotero kuti ana a Israele azidza nazo nsembe zao, zimene aziphera kuthengo koyera, kuti adze nazo kwa Yehova, ku khomo la chihema chokomanako, kwa wansembe, ndi kuziphera nsembe zoyamika za Yehova.


Ndipo chopereka chake chikakhala nkhosa kapena mbuzi, kuti ikhale nsembe yoyamika ya kwa Yehova; ingakhale yaimuna kapena yaikazi, azibwera nayo yopanda chilema;


Anaphanso ng'ombe, ndi nkhosa yamphongoyo, ndizo nsembe zoyamika za anthu; ndi ana a Aroni anapereka kwa iye mwaziwo, ndipo anauwaza paguwa la nsembe pozungulira,


ndi ng'ombe, ndi nkhosa yamphongo zikhale zakuyamika, kuziphera nsembe pamaso pa Yehova; ndi nsembe yaufa yosakaniza ndi mafuta; pakuti lero Yehova wakuonekerani inu.


Inde, mungakhale mupereka kwa Ine nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zaufa, sindidzazilandira Ine; ndi nsembe zoyamika za ng'ombe zanu zonenepa, sindidzazisamalira Ine.


Koma wotembereredwa wonyengayo, wokhala nayo yaimuna m'gulu lake, nawinda, naphera Yehova nsembe chinthu chachilema; pakuti Ine ndine mfumu yaikulu, ati Yehova wa makamu; ndipo dzina langa ndi loopsa pakati pa amitundu.


Ndipo pamene mupereka yakhungu ikhale nsembe, mukuti, Palibe choipa! Ndi popereka yotsimphina ndi yodwala, palibe choipa! Kaiperekeni kwa kazembe wanu, mudzamkomera kodi? Kapena adzakuvomerezani kodi? Ati Yehova wa makamu.


Ndipo pamene mukonza ng'ombe ikhale nsembe yopsereza, kapena yophera, kuchita chowinda cha padera, kapena ikhale nsembe yoyamika ya Yehova;


pamenepo abwere nacho chopereka chake kwa Yehova, nkhosa yamphongo ya chaka chimodzi yopanda chilema, ikhale nsembe yopsereza, ndi nkhosa yaikazi yopanda chilema ikhale nsembe yauchimo, ndi nkhosa yamphongo yopanda chilema ikhale nsembe yoyamika;


ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Nasoni mwana wa Aminadabu.


ndi nsembe yoyamika, ng'ombe ziwiri, nkhosa zamphongo zisanu, atonde asanu, anaankhosa asanu a chaka chimodzi; ndicho chopereka cha Gamaliele mwana wa Pedazuri.


ndipo mupereke nsembe zanu zopsereza, nyama zao ndi mwazi wao, paguwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu; ndipo athire mwazi wa nsembe zanu zophera paguwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu, koma nyama yake muidye.


mwa Iyenso kuyanjanitsa zinthu zonse kwa Iye mwini, atachita mtendere mwa mwazi wa mtanda wake; mwa Iyetu, kapena za padziko, kapena za mu Mwamba.


tiyandikire ndi mtima woona, m'chikhulupiriro chokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuichotsera chikumbumtima choipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera;


chimene tidachiona, ndipo tidachimva, tikulalikirani inunso, kuti inunso mukayanjane pamodzi ndi ife; ndipo chiyanjano chathu chilinso ndi Atate, ndipo ndi Mwana wake Yesu Khristu;


Pamenepo ana onse a Israele ndi anthu onse anakwera nafika ku Betele, nalira misozi, nakhala pansi pomwepo pamaso pa Yehova, nasala chakudya tsiku lomwelo mpaka madzulo; napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika pamaso pa Yehova.


Ndipo kunali m'mawa mwake, anthu analawirira mamawa namangako guwa la nsembe, napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa