Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 3:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo wansembe azitenthe paguwa la nsembe; ndicho chakudya cha nsembe yamoto ya kwa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo wansembe azitenthe pa guwa la nsembe; ndicho chakudya cha nsembe yamoto ya kwa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Tsono wansembe atenthe zonsezo pa guwa, kuti zikhale chakudya chotentha pa moto, chopereka kwa Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Wansembe awotche zonsezi pa guwa. Ichi ndi chakudya chotentha pa moto choperekedwa kwa Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 3:11
17 Mawu Ofanana  

Ndathiridwa pansi monga madzi, ndipo mafupa anga onse anaguluka. Mtima wanga ukunga sera; wasungunuka m'kati mwa matumbo anga.


popeza mwalowa nao achilendo osadulidwa m'mtima, osadulidwa m'thupi akhale m'malo anga opatulika kuwadetsa, ndiwo nyumba yanga, popereka inu mkate wanga, mafuta, ndi mwazi; ndipo munathyola pangano langa pamodzi ndi zonyansa zanu zonse.


Nena ndi Aroni, kuti, Aliyense wa mbeu zako mwa mibadwo yao wakukhala nacho chilema, asayandikize kupereka mkate wa Mulungu wake.


Azikhala opatulikira Mulungu wao, osaipsa dzina la Mulungu wao; popeza amapereka nsembe zamoto za Yehova, mkate wa Mulungu wao; chifukwa chake akhale opatulika.


Chifukwa chake umpatule; popeza amapereka mkate wa Mulungu wako; umuyese wopatulika; pakuti Ine Yehova wakupatula iwe, ndine woyera.


Ndipo musamazilandira izi ku dzanja la mlendo ndi kubwera nazo zikhale chakudya cha Mulungu wanu; popeza zili nako kuvunda kwao; zili ndi chilema; sizidzalandirikira inu.


Ndipo wansembe atenthe izi paguwa la nsembe; ndizo chakudya cha nsembe yamoto ichite fungo lokoma; mafuta onse nga Yehova.


Ndipo ana a Aroni azitenthe paguwa la nsembe, pa nsembe yopsereza, ili pa nkhuni zimene zili pamoto; ndiyo nsembe yamoto, ya fungo lokoma la kwa Yehova.


Koma inu muliipsa, pakunena inu, Gome la Ambuye laipsidwa, ndi zipatso zake, chakudya chake, chonyozeka.


Mupereka mkate wodetsedwa paguwa langa la nsembe; ndipo mukuti, Takudetsani motani? M'menemo, mwakuti munena, Gome la Yehova nlonyozeka.


Uza ana a Israele, nuti nao, Muzisamalira kubwera nacho kwa Ine chopereka changa, chakudya changa cha nsembe zanga zamoto, cha fungo lokoma, pa nyengo yake yoikika.


Momwemo mupereke chakudya cha nsembe yamoto cha fungo lokoma la Yehova, tsiku ndi tsiku, masiku asanu ndi awiri, chakupereka pamodzi ndi nsembe yopsereza yosalekeza, ndi nsembe yake yothira.


Iye amene sanatimane Mwana wake wa Iye yekha, koma anampereka chifukwa cha ife tonse, adzalekeranji kutipatsanso ife zinthu zonse kwaulere pamodzi ndi Iye?


Simungathe kumwera chikho cha Ambuye, ndi chikho cha ziwanda; simungathe kulandirako kugome la Ambuye, ndi kugome la ziwanda.


Taona, ndaima pakhomo, ndigogoda; wina akamva mau anga nakatsegula pakhomo, ndidzalowa kwa iye, ndipo ndidzadya naye, ndi iye ndi Ine.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa