Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 26:8 - Buku Lopatulika

8 Asanu a inu adzapirikitsa zana limodzi, ndi zana limodzi la inu adzapirikitsa zikwi khumi; ndi adani anu adzagwa pamaso panu ndi lupanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Asanu a inu adzapirikitsa zana limodzi, ndi zana limodzi la inu adzapirikitsa zikwi khumi; ndi adani anu adzagwa pamaso panu ndi lupanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Anthu asanu okha mwa inu adzapirikitsa anthu zana ndipo anthu zana mwa inu adzapirikitsa anthu zikwi khumi, ndipo adani anuwo mudzaŵagonjetsa ndi lupanga

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Anthu asanu mwa inu adzapirikitsa anthu 100, ndipo anthu 100 mwa inu adzathamangitsa anthu 10,000, ndipo adani anuwo mudzawagonjetsa ndi lupanga.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 26:8
15 Mawu Ofanana  

Kuwerenga kwa amphamvu aja Davide anali nao ndi uku: Yasobeamu mwana wa Muhakimoni, mkulu wa makumi atatu aja, anasamulira mazana atatu mkondo wake, nawapha nthawi imodzi.


Ndipo Abisai mbale wa Yowabu, ndiye wamkulu wa atatuwa; pakuti anasamulira mazana atatu mkondo wake, nawapha, namveka dzina pakati pa atatuwa.


Nasonkhana pamodzi Ayuda ena okhala m'maiko a mfumu, nalimbikira moyo wao, napumula pa adani ao, nawapha a iwo odana nao zikwi makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu; koma sanalande zofunkha.


Mudzapirikitsa adani anu, ndipo adzagwa pamaso panu ndi lupanga.


Tsiku ilo Yehova adzatchinjiriza okhala mu Yerusalemu; ndi iye wokhumudwa pakati pao tsiku lomwelo adzakhala ngati Davide; ndi nyumba ya Davide idzakhala ngati Mulungu, ngati mthenga wa Yehova pakati pao.


Chokhachi musamapikisana naye Yehova, musamaopa anthu a m'dzikomo; pakuti ndiwo mkate wathu; mthunzi wao wawachokera, ndipo Yehova ali nafe; musamawaopa.


Muwatume kunkhondo a fuko limodzi, chikwi chimodzi, atere mafuko onse a Israele.


Yehova adzakantha adani anu akukuukirani; adzakudzerani njira imodzi, koma adzathawa pamaso panu njira zisanu ndi ziwiri.


Mmodzi akadapirikitsa zikwi, awiri akadathawitsa zikwi khumi, akadapanda kuwagulitsa Thanthwe lao, akadapanda kuwapereka Yehova.


Munthu mmodzi wa inu adzapirikitsa anthu chikwi chimodzi; pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye amathirira inu nkhondo monga ananena ndi inu.


Ndipo anapeza chibwano chatsopano cha bulu, natambasula dzanja lake nachigwira, nakantha nacho amuna chikwi chimodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa