Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 26:3 - Buku Lopatulika

3 Mukamayenda m'malemba anga, ndi kusunga malamulo anga, ndi kuwachita;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Mukamayenda m'malemba anga, ndi kusunga malamulo anga, ndi kuwachita;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 “Mukamayenda motsata njira zanga ndi kumamvera malamulo anga onse ndi kuŵatsatadi,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 “ ‘Mukamayenda motsata malangizo anga ndi kumvera mosamalitsa malamulo anga,

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 26:3
19 Mawu Ofanana  

koma mukabwerera kudza kwa Ine, ndi kusunga malamulo anga, ndi kuwachita, angakhale otayika anu anali ku malekezero a thambo, ndidzawasonkhanitsa kuchokera komweko, ndi kubwera nao kumalo ndinawasankha kukhalitsako dzina langa.


Ndipo muzitumikira Yehova Mulungu wanu, potero adzadalitsa chakudya chako, ndi madzi ako; ndipo ndidzachotsa nthenda pakati pa iwe.


Ngati inu muli ofuna ndi omvera, mudzadya zabwino za dziko,


Ndipo Mulungu adzapatsa mvula ya mbeu yako, ukaibzale m'nthaka; ndi mkate ndiwo phindu la nthaka, ndipo tirigu wake adzacha bwino ndi kuchuluka; tsiku limenelo ng'ombe zako zidzadya m'madambo aakulu.


limene ndinauza makolo anu tsiku lomwe ndinawatulutsa m'dziko la Ejipito, m'ng'anjo ya chitsulo, kuti, Mverani mau anga, ndi kuwachita, monga mwa zonse zimene ndikuuzani inu; ndipo mudzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wanu;


Chaka chachisanu muzidya zipatso zake, kuti zobala zake zikuchulukireni inu; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.


Pakuti padzakhala mbeu ya mtendere; mpesa udzapatsa zipatso zake, ndi nthaka idzapatsa zobala zake, ndi miyamba idzapatsa mame ao; ndipo ndidzalandiritsa otsala a anthu awa izi zonse, chikhale cholowa chao.


Mubwere nalo limodzilimodzi lonse la khumi, kunyumba yosungiramo, kuti m'nyumba mwanga mukhale chakudya; ndipo mundiyese nako tsono, ati Yehova wa makamu, ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoweka malo akuulandira.


Ndipo kudzakhala, chifukwa cha kumvera inu maweruzo awa, ndi kuwasunga, ndi kuwachita, Yehova Mulungu wanu adzakusungirani chipangano ndi chifundo chimene analumbirira makolo anu;


Odala iwo amene atsuka miinjiro yao, kuti akakhale nao ulamuliro pa mtengo wa moyo, ndi kuti akalowe m'mzinda pazipata.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa