Levitiko 2:4 - Buku Lopatulika4 Ndipo ukabwera nacho chopereka ndicho nsembe yaufa, yophika mumchembo, chizikhala cha timitanda ta ufa wosalala topanda chotupitsa tosakaniza ndi mafuta, kapena timitanda taphanthi topanda chotupitsa todzoza ndi mafuta. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Ndipo ukabwera nacho chopereka ndicho nsembe yaufa, yophika mumchembo, chizikhala cha timitanda ta ufa wosalala topanda chotupitsa tosanganiza ndi mafuta, kapena timitanda taphanthi topanda chotupitsa todzoza ndi mafuta. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 “Ukamapereka chopereka cha chakudya chophika mu uvuni, chikhale buledi wa ufa wa tirigu wosalala wopanda chofufumitsira, wosakaniza ndi mafuta, kapena ikhale timitanda ta buledi wosafufumitsa, topyapyala, topaka mafuta. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 “ ‘Ukabweretsa nsembe ya chakudya chophika mu uvuni, ikhale ya buledi wa ufa wosalala wopanda yisiti koma wosakaniza ndi mafuta, kapena timitanda ta buledi topyapyala, topanda yisiti koma topaka mafuta. Onani mutuwo |