Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 2:12 - Buku Lopatulika

12 Monga chopereka cha zipatso zoyamba muzipereka izi kwa Yehova: koma asazifukize paguwa la nsembe zichite fungo lokoma.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Monga chopereka cha zipatso zoyamba muzipereka izi kwa Yehova: koma asazifukize pa guwa la nsembe zichite fungo lokoma.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Ziŵirizo ungathe kubwera nazo ngati nsembe ya zokolola zoyambirira zopereka kwa Chauta. Koma usazitenthere pa guwa kuti zipereke fungo lonunkhira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Ziwirizi ungathe kubwera nazo kwa Yehova ngati chopereka cha zokolola zoyambirira. Koma usazitenthe pa guwa kuti zikhale fungo lokomera Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 2:12
15 Mawu Ofanana  

Ndipo munda wa Efuroni umene unali mu Makipela, umene unali patsogolo pa Mamure, munda ndi phanga lili momwemo, ndi mitengo yonse inali m'mundamo, yokhala m'malire monse mozungulira momwemo,


Ndipo pobuka mau aja, ana a Israele anapereka mochuluka, zobala zoyamba za tirigu, vinyo, ndi mafuta, ndi uchi, ndi za zipatso zonse za m'minda, ndi limodzi la magawo khumi la zonse anabwera nazo mochuluka.


Usachedwa kuperekako zipatso zako zochuluka, ndi zothira zako. Woyamba wa ana ako aamuna undipatse Ine.


Uzibwera nazo zoyambayamba za m'munda mwako kunyumba ya Yehova Mulungu wako. Usaphike mwanawambuzi mu mkaka wa make.


Ndipo uzichita chikondwerero cha Masabata, ndicho chikondwerero cha Zipatso zoyamba za Masika a tirigu, ndi chikondwerero cha Kututa pakutha pa chaka.


Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mutakalowa m'dziko limene ndikupatsani, ndi kucheka dzinthu zake, pamenepo muzidza nao mtolo wa zipatso zoyamba za masika anu kwa wansembe;


Mutuluke nayo m'zinyumba zanu mikate iwiri ya nsembe yoweyula, ikhale ya awiri a magawo khumi a efa; ikhale ya ufa wosalala, yopanga ndi chotupitsa, zipatso zoyamba za Yehova.


Abwere nacho chopereka chake pamodzi ndi timitanda ta mkate wachotupitsa, pamodzi ndi nsembe yolemekeza, ya nsembe zoyamika zake.


Pa mtanda wanu woyamba muperekeko kamtanda, kakhale nsembe yokweza; monga mumachitira nsembe yokweza ya popuntha tirigu, momwemo muzikakweza,


Mafuta onse okometsetsa, ndi vinyo watsopano, ndi tirigu yense wokometsetsa. Zipatso zao zoyamba zimene aziperekako kwa Yehova, ndazipereka kwa iwe.


Koma tsopano Khristu waukitsidwa kwa akufa, chipatso choyamba cha iwo akugona.


Ndipo tsopano, taonani, ndabwera nazo zoyamba za zipatso za nthaka, zimene Inu, Yehova, mwandipatsa. Ndipo muziike pamaso pa Yehova Mulungu wanu;


Iwo ndiwo amene sadetsedwa pamodzi ndi akazi; pakuti ali anamwali. Iwo ndiwo amene atsata Mwanawankhosa kulikonse amukako. Iwowa anagulidwa mwa anthu, zipatso zoyamba kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa