Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 2:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo chopereka chako chilichonse cha nsembe yaufa uzichikoleretsa ndi mchere; usasowe mchere wa chipangano cha Mulungu wako pa nsembe yako yaufa; pa zopereka zako zonse uzipereka mchere.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo chopereka chako chilichonse cha nsembe yaufa uzichikoleretsa ndi mchere; usasowe mchere wa chipangano cha Mulungu wako pa nsembe yako yaufa; pa zopereka zako zonse uzipereka mchere.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Zopereka zako zonse za zakudya uzithire mchere, osaiŵala ai: mcherewo ndi wosonyeza chipangano cha pakati pa iwe ndi Mulungu wako. Uzithira mchere nsembe zako zonse.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Zopereka zako zonse zachakudya uzithire mchere. Usayiwale kuthira mchere pa chopereka chako popeza mcherewo ukusonyeza pangano pakati pa iwe ndi Mulungu wako. Tsono uzinthira mchere pa chopereka chako chilichonse.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 2:13
8 Mawu Ofanana  

simudziwa kodi kuti Yehova Mulungu wa Israele anapereka chiperekere ufumu wa Israele kwa Davide, kwa iye ndi ana ake, ndi pangano lamchere?


mpaka matalente a siliva zana limodzi, ndi miyeso ya tirigu zana limodzi, ndi mitsuko ya vinyo zana limodzi, ndi mitsuko ya mafuta zana limodzi, ndi mchere wosauwerenga.


ndipo uzikonza nazo chofukiza, chosakaniza mwa machitidwe a wosakaniza, chokometsera ndi mchere, choona, chopatulika;


Ndipo ubwere nazo kwa Yehova, ndi ansembe athirepo mchere, ndi kuzipereka nsembe yopsereza ya Yehova.


Nsembe zokweza zonse za zinthu zopatulika, zimene ana a Israele azikweza kwa Yehova, ndazipereka kwa iwe, ndi kwa ana ako aamuna ndi kwa ana ako aakazi pamodzi ndi iwe, likhale lemba losatha; ndilo pangano lamchere losatha, pamaso pa Yehova, kwa iwe ndi mbeu zako pamodzi ndi iwe.


Inu ndinu mchere wa dziko lapansi; koma mcherewo ngati ukasukuluka, adzaukoleretsa ndi chiyani? Pamenepo sungakwanirenso kanthu konse, koma kuti ukaponyedwe kunja, nupondedwe ndi anthu.


Mau anu akhale m'chisomo, okoleretsa, kuti mukadziwe inu mayankhidwe anu a kwa yense akatani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa