Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 13:5 - Buku Lopatulika

5 ndipo wansembe amuonenso tsiku lachisanu ndi chiwiri; ndipo taonani, monga momwe apenyera iye, nthenda yaima, nthenda siinapitirire pakhungu, pamenepo wansembe ambindikiritsenso masiku asanu ndi awiri ena;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 ndipo wansembe amuonenso tsiku lachisanu ndi chiwiri; ndipo taonani, monga momwe apenyera iye, nthenda yaima, nthenda siinapitirira pakhungu, pamenepo wansembe ambindikiritsenso masiku asanu ndi awiri ena;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Wansembe amuwonetsetse wodwalayo pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri. Akaiwona nthendayo kuti sidafalikire pa khungu, pamenepo wansembeyo amtsekere munthu uja masiku asanu ndi aŵiri ena.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri wansembe amuonenso bwino wodwalayo. Ndipo ngati waona kuti nthendayo sinasinthe ndipo sinafalikire pa khungu, amuyikenso wodwalayo padera kwa masiku ena asanu ndi awiri.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 13:5
4 Mawu Ofanana  

mwana wake wamwamuna amene adzakhala wansembe m'malo mwake azivala masiku asanu ndi awiri, pakulowa iye m'chihema chokomanako kutumikira m'malo opatulika.


Koma ngati chikanga chikhala chotuwa pa khungu la thupi lake, ndipo chikaoneka chosapitirira khungu, ndi tsitsi lake losasanduka loyera, pamenepo wansembe ambindikiritse wanthendayo masiku asanu ndi awiri;


ndipo wansembe amuonenso tsiku lachisanu ndi chiwiri, ndipo taonani, nthenda yazimba yosapitirira khungu nthendayi, pamenepo wansembe amutche iye woyera, ndiyo nkhanambo chabe; ndipo atsuke zovala zake, ndiye woyera;


Ndipo iye wakuti ayeretsedwe atsuke zovala zake, namete tsitsi lake lonse, nasambe madzi, nakhale woyera; ndipo atatero alowe kuchigono, koma agone pa bwalo la hema wake masiku asanu ndi awiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa