Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 13:6 - Buku Lopatulika

6 ndipo wansembe amuonenso tsiku lachisanu ndi chiwiri, ndipo taonani, nthenda yazimba yosapitirira khungu nthendayi, pamenepo wansembe amutche iye woyera, ndiyo nkhanambo chabe; ndipo atsuke zovala zake, ndiye woyera;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 ndipo wansembe amuonenso tsiku lachisanu ndi chiwiri, ndipo taonani, nthenda yazimba yosapitirira khungu nthendayi, pamenepo wansembe amutche iye woyera, ndiyo nkhanambo chabe; ndipo atsuke zovala zake, ndiye woyera;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Tsono wansembe uja amuwonetsetsenso wodwalayo pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri. Pakhungu pakakhala pothimbirira, nthendayo yosafalikira pakhungupo, wansembe amutchule munthuyo kuti ndi wosaipitsidwa. Umenewo ndi m'buko chabe, tsono wodwalayo achape zovala zake, ndipo adzakhala woyeretsedwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri wansembeyo amuonenso bwino munthuyo, ndipo ngati nthendayo yazima ndi kusafalikira pa khungu, wansembe amutchule munthuyo kuti ndi woyera. Umenewo unali mʼbuko chabe. Choncho munthuyo achape zovala zake ndipo adzakhala woyera.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 13:6
23 Mawu Ofanana  

tsono pempho ndi pembedzero lililonse akalipempha munthu aliyense, kapena anthu anu onse Aisraele, pakuzindikira munthu yense chinthenda cha mtima wa iye yekha, ndi kutambasulira manja ake kunyumba ino;


pamenepo mverani Inu mu Mwamba pempho ndi pembedzero lao, ndi kulimbitsa mlandu wao.


Adziwitsa zolowereza zake ndani? Mundimasule kwa zolakwa zobisika.


Ndani anganene, Ndasambitsa mtima wanga, ndayera opanda tchimo?


Pakuti kulibe wolungama pansi pano amene achita zabwino osachimwa.


Bango lophwanyika sadzalithyola, ndi lawi lozilala sadzalizima; adzatulutsa chiweruzo m'zoona.


ndipo aliyense akanyamulako nyama ya mtembo wake azitsuka zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.


Ndipo iye amene akanyamula mtembo wake atsuke zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; muziyese izi zodetsa.


Ndipo iye wakudya kanthu ka mtembo wake azitsuka zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo; iyenso wakunyamula mtembo wake atsuke zovala zake, nadzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.


Ngati munthu ali nacho chotupa, kapena nkhanambo, kapena chikanga pa khungu la thupi lake, ndipo isandulika nthenda yakhate pa khungu la thupi lake, azifika kwa Aroni wansembe, kapena kwa mmodzi wa ana ake ansembe;


ndipo wansembe amuonenso tsiku lachisanu ndi chiwiri; ndipo taonani, monga momwe apenyera iye, nthenda yaima, nthenda siinapitirire pakhungu, pamenepo wansembe ambindikiritsenso masiku asanu ndi awiri ena;


koma nkhanambo ikapitirira khungu, atadzionetsa kwa wansembe kuti atchedwe woyera, adzionetsenso kwa wansembe;


Ndipo iye wakuti ayeretsedwe atsuke zovala zake, namete tsitsi lake lonse, nasambe madzi, nakhale woyera; ndipo atatero alowe kuchigono, koma agone pa bwalo la hema wake masiku asanu ndi awiri.


Ndipo iye amene ali wofooka m'chikhulupiriro, mumlandire, koma si kuchita naye makani otsutsana ai.


Pokhala nao tsono malonjezano amenewa, okondedwa, tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m'kuopa Mulungu.


Anamchitira zovunda si ndiwo ana ake, chilema nchao; iwo ndiwo mbadwo wopulukira ndi wokhotakhota.


tiyandikire ndi mtima woona, m'chikhulupiriro chokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuichotsera chikumbumtima choipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera;


Popeza akhala zoikika za thupi zokha (ndi zakudya, ndi zakumwa, ndi masambidwe osiyanasiyana), oikidwa kufikira nthawi yakukonzanso.


Pakuti timakhumudwa tonse pa zinthu zambiri. Munthu akapanda kukhumudwa pa mau, iye ndiye munthu wangwiro, wokhoza kumanganso thupi lonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa