Levitiko 10:6 - Buku Lopatulika6 Ndipo Mose anati kwa Aroni, ndi kwa Eleazara ndi Itamara ana ake, Musawinda tsitsi, musang'amba zovala zanu; kuti mungafe, ndi kuti angakwiye Iye ndi khamu lonse; koma abale anu, mbumba yonse ya Israele, alire chifukwa cha motowu Yehova anauyatsa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Ndipo Mose anati kwa Aroni, ndi kwa Eleazara ndi Itamara ana ake, Musawinda tsitsi, musang'amba zovala zanu; kuti mungafe, ndi kuti angakwiye Iye ndi khamu lonse; koma abale anu, mbumba yonse ya Israele, alire chifukwa cha motowu Yehova anauyatsa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Tsono Mose adauza Aroni ndi ana ake Eleazara ndi Itamara kuti, “Musalilekerere tsitsi lanu, ndipo musang'ambe zovala zanu, kuti mungafe, ndiponso kuti mkwiyo ungagwere mpingo wonse. Koma abale anu a m'fuko lonse la Israele ndiwo alire chifukwa cha imfa ya moto umene Chauta watentha nawo anzanu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Ndipo Mose anawuza Aaroni ndi ana ake Eliezara ndi Itamara kuti, “Musalileke tsitsi lanu nyankhalala ndipo musangʼambe zovala zanu kuti mungafe, ndi mkwiyo wa Yehova ungagwere anthu onsewa. Koma abale anu okha, kutanthauza fuko lonse la Israeli ndiwo ayenera kulira omwalira aja amene Yehova wawapsereza ndi moto. Onani mutuwo |