Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 1:2 - Buku Lopatulika

2 Lankhula ndi ana a Israele, nunene nao, Aliyense mwa inu akabwera nacho chopereka cha kwa Yehova, muzibwera nacho chopereka chanu chikhale cha zoweta, cha ng'ombe, kapena cha nkhosa, kapena cha mbuzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Lankhula ndi ana a Israele, nunene nao, Aliyense mwa inu akabwera nacho chopereka cha kwa Yehova, muzibwera nacho chopereka chanu chikhale cha zoweta, cha ng'ombe, kapena cha nkhosa, kapena cha mbuzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 “Uza Aisraele kuti, ‘Munthu aliyense akamabwera ndi chopereka kwa Chauta, azitenga ng'ombe kapena nkhosa kapena mbuzi.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 “Aliyense wa inu ngati abwera ndi nsembe kwa Yehova kuchokera pa ziweto zake, choperekacho chikhale ngʼombe, nkhosa kapena mbuzi.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 1:2
13 Mawu Ofanana  

Ndipo panali atapita masiku, Kaini anatenga zipatso za nthaka, nsembe ya kwa Yehova.


koma sanayang'anire Kaini ndi nsembe yake. Kaini ndipo anakwiya kwambiri, ndipo nkhope yake inagwa.


Mchitireni Yehova ulemerero wa dzina lake; bwerani nacho chopereka, ndipo fikani pamaso pake; lambirani Yehova m'chiyero chokometsetsa.


atatero anaperekanso nsembe yopsereza yosalekeza, ndi za pokhala mwezi, ndi za nyengo zoikika zonse za Yehova zopatulika, ndi za munthu yense wopereka nsembe yaufulu kwa Yehova mwaufulu.


Undiumbire guwa la nsembe ladothi, nundiphere pomwepo nsembe zako zopsereza, ndi nsembe zako zamtendere, nkhosa zako ndi ng'ombe zako; paliponse ndikumbukiritsa anthu dzina langa ndidzakudzera ndi kukudalitsa.


ndipo mukakonzera Yehova nsembe yamoto, nsembe yopsereza, kapena yophera, pochita chowinda cha padera, kapena nsembe yaufulu, kapena nsembe ya pa nyengo zanu zoikika, kumchitira Yehova fungo lokoma, la ng'ombe kapena nkhosa;


pamenepo mwamunayo azidza naye mkazi wake kwa wansembe, nadze nacho chopereka chake, limodzi la magawo khumi la efa wa ufa wabarele; asathirepo mafuta, kapena kuikapo lubani; popeza ndiyo nsembe yaufa yansanje, nsembe yaufa yachikumbutso, yakukumbutsa mphulupulu.


ng'ombe yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi, mwanawankhosa mmodzi wa chaka chimodzi, zikhale nsembe yopsereza;


koma inu munena, Munthu akati kwa atate wake, kapena amai wake, Korban, ndiko kuti Mtulo, chimene ukadathandizidwa nacho ndi ine,


Chifukwa chake ndikupemphani inu, abale, mwa zifundo za Mulungu, kuti mupereke matupi anu nsembe yamoyo, yopatulika, yokondweretsa Mulungu, ndiko kupembedza kwanu koyenera.


Ndipo pokhala ife ndi mphatso zosiyana, monga mwa chisomo chipatsidwa kwa ife, kapena mphatso yakunenera, tinenere monga mwa muyeso wa chikhulupiriro;


ndipo yendani m'chikondi monganso Khristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa