Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Hoseya 4:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo udzakhumudwa usana, ndi mneneri yemwe adzakhumudwa pamodzi ndi iwe usiku; ndipo ndidzaononga mai wako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo udzakhumudwa usana, ndi mneneri yemwe adzakhumudwa pamodzi ndi iwe usiku; ndipo ndidzaononga mai wako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Mumakhumudwa usana ndi usiku, ndipo aneneri nawonso amachita chimodzimodzi, motero ndidzaononga Israele mai wanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Mumapunthwa usana ndi usiku ndipo aneneri amapunthwa nanu pamodzi. Choncho ndidzawononga amayi anu.

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 4:5
21 Mawu Ofanana  

Atero Yehova, Kalata ya chilekaniro cha amai ako ali kuti amene ndinamsudzula naye? Pena ndani wa angongole anga amene ndamgulitsa iwe? Taona chifukwa cha zoipa zanu munagulitsidwa, ndi chifukwa cha kulakwa kwanu amanu anachotsedwa.


Amasiye ao andichulukira Ine kopambana mchenga wa kunyanja; ndatengera wofunkha usana afunkhire mai wao wa anyamata; ndamgwetsera dzidzidzi kuwawa mtima ndi mantha.


Za aneneri. Mtima wanga usweka m'kati mwanga, mafupa anga onse anthunthumira; ndinga munthu woledzera, ngati munthu amene vinyo anamposa; chifukwa cha Yehova, ndi chifukwa cha mau ake opatulika.


amai anu adzakhala ndi manyazi ambiri; amene anakubalani adzathedwa nzeru; taonani, adzakhala wapambuyo wa amitundu, chipululu, dziko louma, bwinja.


Wobadwa ndi munthu iwe, anthu awa anautsa mafano ao mumtima mwao, naimika chokhumudwitsa cha mphulupulu yao pamaso pao; ndifunsidwe nao konse kodi?


Mutsutsane naye mai wanu, mutsutsane naye; pakuti sali mkazi wanga, ndi Ine sindili mwamuna wake; ndipo achotse zadama zake pankhope pake, ndi zigololo zake pakati pa mawere ake;


Pakuti mai wao anachita chigololo; iye amene anali ndi pakati pa iwo anachita chamanyazi; pakuti anati, Ndidzatsata ondikondawo, akundipatsa ine chakudya changa, ndi madzi anga, ubweya wanga, ndi thonje langa, mafuta anga, ndi chakumwa changa.


Ndipo kudzikuza kwa Israele kudzamchitira umboni pamaso pake; chifukwa chake Israele ndi Efuremu adzakhumudwa m'mphulupulu mwao; Yudanso adzakhumudwa pamodzi nao.


Ndipo ndinatha abusa atatuwo mwezi umodzi; pakuti mtima wanga unalema nao, ndi mtima waonso unaipidwa nane.


Ndipo kudzachitika tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, ndidzaononga maina a mafano m'dziko; ndipo sadzakumbukikanso; ndipo ndidzachotsa m'dziko aneneri ndi mzimu wachidetso.


Koma Yerusalemu wa kumwamba uli waufulu, ndiwo amai wathu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa