Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 6:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo anati Yehova, Ndidzafafaniza anthu amene ndawalenga padziko lapansi; anthu, ndi nyama, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga: pakuti ndimva chisoni chifukwa ndapanga izo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo anati Yehova, Ndidzafafaniza anthu amene ndawalenga pa dziko lapansi; anthu, ndi nyama, ndi zokwawa, ndi mbalame za m'mlengalenga: pakuti ndimva chisoni chifukwa ndapanga izo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Tsono adati, “Anthu onse amene ndaŵalenga, ndidzaŵaononga kotheratu. Ndidzaononganso nyama zonse ndi zokwaŵa zomwe pamodzi ndi mbalame, chifukwa ndikumva chisoni kuti ndidalenga zimenezi.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Choncho Yehova anati, “Ndidzafafaniza munthu, nyama, zonse zokwawa, ndi mbalame za mu mlengalenga pa dziko lapansi, pakuti ndikumva chisoni kuti ndinazilenga zimenezi.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 6:7
21 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anamva chisoni chifukwa anapanga munthu padziko lapansi, ndipo anavutika m'mtima mwake.


Ndipo zinafa zamoyo zonse zoyenda padziko lapansi, zouluka, ndi nyama, ndi zamoyo, ndi zokwawa zonse zakukwawa padziko lapansi, ndi anthu onse:


Pakuti akapita masiku asanu ndi awiri Ine ndidzavumbitsa mvula padziko lapansi masiku makumi anai usana ndi usiku; ndi zinthu zamoyo zonse zomwe ndazipanga ndidzaziononga padziko lapansi.


Ndipo Yehova anamva chonunkhira chakukondweretsa; nati Yehova m'mtima mwake, Sindidzatembereranso konse nthaka chifukwa cha munthu; pakuti ndingaliro ya mtima wa munthu ili yoipa kuyambira pa unyamata wake; sindidzaphanso konse zinthu zonse zamoyo, monga momwe ndachitiramo.


Pakuti oipa adzatayika, ndipo adani ake a Yehova adzanga mafuta a anaankhosa; adzanyeka, monga utsi adzakanganuka.


Kuopa Yehova kutanimphitsa masiku; koma zaka za oipa zidzafinimpha.


Zonse Yehova anazipanga zili ndi zifukwa zao; ngakhale amphulupulu kuti aone tsiku loipa.


Ponyala nthambi zake zidzathyoledwa; akazi adzafika, nazitentha ndi moto, pakuti ali anthu opanda nzeru; chifukwa chake Iye amene anawalenga sadzawachitira chisoni, ndi Iye amene anawaumba sadzawakomera mtima.


Chifukwa chake dziko lidzachita chisoni, ndi aliyense wokhalamo adzalefuka, pamodzi ndi nyama zakuthengo, ndi mbalame za m'mlengalenga; ndi nsomba za m'nyanja zomwe zidzachotsedwa.


Ndipo Yehova anachileka. Sichidzachitika, ati Yehova.


Ndipo Yehova anachileka. Ichi chomwe sichidzachitika, ati Ambuye Yehova.


Ngakhale siliva wao, ngakhale golide wao sizidzakhoza kuwalanditsa tsiku la mkwiyo wa Yehova; koma dziko lonse lidzatha ndi moto wa nsanje yake; pakuti adzachita chakutsiriza, mofulumira, onse okhala m'dziko.


Kuzitha ndidzazitha zonse kuzichotsa panthaka, ati Yehova.


Ndidzatha munthu ndi nyama; ndidzatha mbalame za m'mlengalenga, ndi nsomba za m'nyanja, ndi zokhumudwitsa pamodzi ndi oipa; ndipo ndidzaononga anthu kuwachotsa panthaka, ati Yehova.


Ndipo kudzali kuti, monga Yehova anakondwera nanu kukuchitirani zabwino, ndi kukuchulukitsani; momwemo Yehova adzakondwera nanu kutayikitsa ndi kuononga inu, ndipo adzakuzulani kudziko kumene mulowako kulilandira.


Yehova sadzamkhululukira, koma pamenepo mkwiyo wa Yehova ndi nsanje yake zidzamfukira munthuyo; ndipo temberero lonse lolembedwa m'buku ili lidzamkhalira; ndipo Yehova adzafafaniza dzina lake pansi pa thambo.


Kundichititsa chisoni kuti ndinaika Saulo akhale mfumu; pakuti wabwerera wosanditsata Ine, ndipo sanachite malamulo anga. Ndipo Samuele anakwiya; nalira kwa Yehova usiku wonse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa