Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 50:21 - Buku Lopatulika

21 Ndipo tsopano musaope; ine ndidzachereza inu, ndi ana anu aang'ono. Ndipo anawatonthoza iwo mitima yao, nanena nao mokoma mtima.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Ndipo tsopano musaope; ine ndidzachereza inu, ndi ana anu ang'ono. Ndipo anawatonthoza iwo mitima yao, nanena nao mokoma mtima.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Tsopano inu musade nkhaŵa. Ndidzakusamalani pamodzi ndi ana anu omwe.” Motero adaŵalimbitsa mtima naŵasangulutsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Kotero, musachite mantha. Ine ndidzasamalira inu pamodzi ndi ana anu omwe.” Tsono iye anawalimbitsa mtima powayankhula moleza mtima.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 50:21
13 Mawu Ofanana  

Ndipo mtima wake unakhumba Dina mwana wake wamkazi wa Yakobo, ndipo anamkonda namwaliyo, nanena momkopa namwaliyo.


Tsopano musapwetekwe mtima, musadzikwiyira inu nokha, kuti munandigulitsa ine kuno, pakuti Mulungu ananditumiza ine patsogolo panu kuti ndisunge moyo.


Ndipo Yosefe anachereza atate wake ndi abale ake, ndi mbumba yonse ya atate wake ndi chakudya monga mwa mabanja ao.


Ndipo Yosefe anakhala mu Ejipito, iye, ndi mbumba ya atate wake; ndipo Yosefe anakhala ndi moyo zaka zana limodzi ndi khumi.


Ndipo Hezekiya ananena motonthoza mtima kwa Alevi onse akuzindikira bwino za utumiki wa Yehova. Ndipo anadya pamkomano masiku asanu ndi awiri, naphera nsembe zoyamika, ndi kulemekeza Yehova Mulungu wa makolo ao.


Munene inu zotonthoza mtima kwa Yerusalemu, nimufuulire kwa iye, kuti nkhondo yake yatha, kuti kuipa kwake kwakhululukidwa; kuti iye walandira mowirikiza m'dzanja la Yehova, chifukwa cha machimo ake onse.


koma Ine ndinena kwa inu, Kondanani nao adani anu, ndi kupempherera iwo akuzunza inu;


Pakuti ngati mukhululukira anthu zolakwa zao adzakhululukira inunso Atate wanu wa Kumwamba.


Penyani kuti wina asabwezere choipa womchitira choipa; komatu nthawi zonse mutsatire chokoma, kwa anzanu, ndi kwa onse.


osabwezera choipa ndi choipa, kapena chipongwe ndi chipongwe, koma penatu madalitso; pakuti kudzatsata ichi mwaitanidwa, kuti mukalandire dalitso.


Koma anauka mwamuna wake namtsata kukamba naye zamtima, kumbwezanso; napita ndi mnyamata wake, ndi abulu awiri. Ndipo mkaziyo anadza naye kunyumba ya atate wake. Ndipo pakumuona atate wa mkaziyo anakondwera kukomana naye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa