Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 46:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo Yakobo anachoka ku Beereseba, ndipo ana aamuna a Israele anamnyamula Yakobo atate wao, ndi ana ao aang'ono, ndi akazi ao, m'magaleta amene Farao anatumiza kuti amnyamule iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo Yakobo anachoka ku Beereseba, ndipo ana amuna a Israele anamnyamula Yakobo atate wao, ndi ana ao ang'ono, ndi akazi ao, m'magaleta amene Farao anatumiza kuti amnyamule iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Tsono Yakobe adanyamuka kuchoka ku Beereseba. Ana ake a Israele aja adakweza bambo wao Yakobe, pamodzi ndi akazi ndi ana, pa ngolo zimene Farao adaatumiza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Yakobo anachoka ku Beeriseba, ndipo ana ake anakweza abambo awo, ana awo, pamodzi ndi akazi awo pa ngolo zimene Farao anatumiza kuti adzakwerepo.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 46:5
9 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa, natenga mkate ndi thumba la madzi, nampatsa Hagara, naika paphewa pake, ndi mwana, namchotsa iye: ndipo iye anamuka, nasocherera m'chipululu cha Beereseba.


Tsopano mwalamulidwa chitani ichi; muwatengere ana anu ndi akazi magaleta a m'dziko la Ejipito; nimubwere naye atate wanu.


Ndipo ana a Israele anachita chotero: ndipo Yosefe anawapatsa iwo magaleta monga analamulira Farao, nawapatsa phoso la panjira.


Ndipo anamfotokozera iye mau onse a Yosefe amene ananena ndi iwo; ndipo pamene anaona magaleta amene Yosefe anatumiza kuti amtengeremo, mtima wa Yakobo atate wao unatsitsimuka;


Ndipo Farao anaitana Mose, nati, Mukani, tumikirani Yehova; nkhosa zanu ndi ng'ombe zanu zokha zitsale; mumuke nao ana anu aang'ononso.


Zoweta zathu zomwe tidzapita nazo; chosatsala chiboda chimodzi; pakuti mwa izo tiyenera kutenga zakutumikira nazo Yehova Mulungu wathu; ndipo tisanafikeko, sitidziwa umo tidzamtumikira Yehova.


Ndipo Yakobo anatsikira ku Ejipito; ndipo anamwalira, iye ndi makolo athu;


Pamene Yakobo anafika ku Ejipito, ndi makolo anu anapemphera kwa Yehova, Yehova anatumiza Mose ndi Aroni, amene anatulutsa makolo anu mu Ejipito, nawakhalitsa pamalo pano.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa